3 Mlonda amamutsekulira khomo, ndipo nkhosa zimamvera mawu ake. Iye amaziyitana mayina nkhosa zakezo, nazitulutsa. 4 Akazitulutsa nkhosa zake zonse, iye amazitsogolera, ndipo nkhosa zakezo zimamutsata chifukwa zimadziwa mawu ake. 5 Koma nkhosazo sizidzatsatira mlendo. Izo zidzamuthawa chifukwa sizizindikira mawu a mlendo."
14 "Ine ndine mʼbusa wabwino. Ine ndimazidziwa nkhosa zanga ndipo nkhosa zangazo zimandidziwa,
27 Nkhosa zanga zimamva mawu anga, Ine ndimazidziwa, ndipo zimanditsata Ine.