Pular para o conteúdo
Publicidade

João 11

21 Marita anati kwa Yesu, "Ambuye, mukanakhala muli kuno, mlongo wanga sakanamwalira. 22 Koma ine ndikudziwa kuti ngakhale tsopano Mulungu adzakupatsani chilichonse chimene mudzamupempha."

23 Yesu anati kwa iye, "Mlongo wako adzauka."

24 Marita anayankha kuti, "Ine ndikudziwa kuti adzauka pa kuukanso pa tsiku lomaliza."

25 Yesu anati kwa iye, "Ine ndine kuuka ndi moyo. Wokhulupirira Ine, angakhale amwalira adzakhala ndi moyo. 26 Aliyense amene ali ndi moyo ndi kukhulupirira Ine sadzamwalira. Kodi iwe ukukhulupirira izi?"

27 Marita anamuwuza Iye kuti, "Inde Ambuye, ine ndikukhulupirira kuti ndinu Khristu, Mwana wa Mulungu, amene abwera mʼdziko lapansi."

Veja também