Pular para o conteúdo
Publicidade

João 12

Yesu Alowa mu Yerusalemu

12 Tsiku lotsatira, gulu lalikulu la anthu lomwe linabwera kuphwando linamva kuti Yesu anali mʼnjira kupita ku Yerusalemu. 13 Iwo anatenga nthambi za kanjedza ndi kupita kukakumana naye, akufuwula kuti,

"Hosana!

"Wodala Iye amene akubwera mʼdzina la Ambuye!

"Yodala Mfumu ya Israeli!"

14 Yesu anapeza bulu wamngʼono ndi kukwerapo, monga kunalembedwa kuti:

15 "Usachite mantha mwana wamkazi wa Ziyoni;

taona mfumu yako ikubwera,

itakhala pa mwana wabulu."

16 Poyamba ophunzira ake sanamvetsetse zonsezi. Koma pomwe Yesu analemekezedwa ndi pamene anazindikira kuti zinthu izi zinalembedwa ndipo kuti anamuchitira Iye.

17 Tsopano gulu la anthu lomwe linali naye pa nthawi imene amaukitsidwa Lazaro ku manda linapitiriza kuchitira umboni. 18 Anthu ambiri, anapita kukakumana naye, chifukwa iwo anamva kuti Iye anachita chizindikiro chodabwitsachi. 19 Choncho Afarisi anati kwa wina ndi mnzake, "Taonani, palibe chimene mwachitapo. Anthu onse akumutsatira Iye!"

Veja também