Pular para o conteúdo
Publicidade

João 13

Yesu Asambitsa Mapazi a Ophunzira Ake

1 Inali pafupifupi nthawi ya phwando la Paska. Yesu anadziwa kuti nthawi yafika yoti achoke mʼdziko lapansi ndi kupita kwa Atate. Atawakonda ake amene anali mʼdziko lapansi, Iye anawaonetsa chikondi chake chonse.

2 Atayamba kudya mgonero, mdierekezi anali atalowa kale mu mtima wa Yudasi Isikarioti mwana wa Simoni, kuti amupereke Yesu. 3 Yesu podziwa kuti Atate anamupatsa Iye zonse mʼmanja mwake, ndi kuti Iye anachokera kwa Mulungu ndipo amabwerera kwa Mulunguyo; 4 anayimirira kuchoka pa chakudya navula zovala zake natenga nsalu yopukutira nadzimanga mʼchiwuno mwake. 5 Atachita izi, anathira madzi mʼbeseni ndi kuyamba kusambitsa mapazi a ophunzira ake, ndi kuwapukuta ndi chopukutira chimene anachimanga mʼchiwuno mwake.

6 Atafika pa Petro, Petroyo anati kwa Iye, "Ambuye, kodi mudzandisambitsa mapazi anga?"

7 Yesu anayankha kuti, "Iwe sukuzindikira tsopano chimene ndikuchita, koma udzazindikira mʼtsogolo."

8 Petro anati, "Ayi, Inu simudzandisambitsa konse mapazi anga."

Yesu anayankha kuti, "Ngati Ine sindisambitsa mapazi ako, ulibe gawo mwa Ine."

9 Simoni Petro anayankha kuti, "Ambuye, osati mapazi okha komanso manja anga ndi mutu wanga womwe!"

10 Yesu anayankha kuti, "Munthu amene wasamba amangofunika kusamba mapazi ake okha chifukwa thupi lake lonse ndi loyera. Ndipo inu ndinu oyera, ngakhale kuti si aliyense mwa inu." 11 Pakuti Iye anadziwa amene adzamupereka, ndipo nʼchifukwa chake anati saliyense wa inu ali woyera.

12 Iye atamaliza kusambitsa mapazi awo anavala zovala zake ndi kubwerera pamalo pake. Iye anawafunsa kuti, "Kodi mukuzindikira zimene ndakuchitirani inu? 13 Inu mumanditcha Ine, Mphunzitsindi Mbuye,ndipo mumakhoza mukamatero, pakuti ichi ndi chimene Ine ndili. 14 Tsono ngati Ine, Mbuye wanu ndi Mphunzitsi wanu, ndasambitsa mapazi anu, inunso muyenera kusambitsana mapazi anu. 15 Ine ndakupatsani chitsanzo kuti muzichita monga Ine ndachitira. 16 Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti wantchito saposa mbuye wake, kapena wotumidwa kuposa amene wamutuma. 17 Ngati inu mudziwa zinthu zimenezi, mudzakhala odala mukamazichita.

Veja também