Yesu Atonthoza Ophunzira Ake
1 "Mtima wanu usavutike. Khulupirirani Mulungu; khulupirirani Inenso. 2 Mʼnyumba mwa Atate anga muli zipinda zambiri. Kukanakhala kuti mulibemo ndikanakuwuzani. Ine ndikupita kumeneko kukakukonzerani malo. 3 Ndipo ndikapita kukakukonzerani malo, ndidzabweranso kudzakutengani, kuti kumene kuli Ineko, inunso mukakhale komweko.