16 Ine ndidzapempha Atate, ndipo adzakupatsani Nkhoswe ina kuti izikhala nanu nthawi zonse. 17 Nkhosweyo ndiye Mzimu wachoonadi. Dziko lapansi silingalandire Nkhosweyi chifukwa samuona kapena kumudziwa. Koma inu mumamudziwa pakuti amakhala nanu ndipo adzakhala mwa inu. 18 Ine sindikusiyani nokha kuti mukhale ana amasiye. Ine ndidzabweranso kwa inu.