10 Pilato anati, "Kodi ukukana kundiyankhula ine? Kodi sukuzindikira kuti ine ndili ndi mphamvu yokumasula ndiponso mphamvu yokupachika?"
11 Yesu anayankha kuti, "Inu simukanakhala ndi mphamvu pa Ine akanapanda kukupatsani kumwamba. Nʼchifukwa chake amene wandipereka Ine kwa inu ndiye wochimwa kwambiri."