Publicidade

João 19

23 Asilikali atamupachika Yesu, anatenga zovala zake ndi kuzigawa zigawo zinayi, gawo limodzi la aliyense wa iwo, ndi kutsala mwinjiro wamʼkati wokha. Chovala ichi chinawombedwa kuyambira pamwamba mpaka pansi wopanda msoko.

24 Iwo anati kwa wina ndi mnzake, "Tiyeni tisachingʼambe koma tichite maere kuti tione amene achitenge."

Izi zinachitika kuti malemba akwaniritsidwe amene anati,

"Iwo anagawana zovala zanga pakati pawo

ndi kuchita maere pa zovala zangazo."

Choncho izi ndi zimene asilikali anachita.

25 Pafupi ndi mtanda wa Yesu panayima amayi ake, mngʼono wa amayi ake, Mariya mkazi wa Kaliyopa ndi Mariya wa ku Magadala. 26 Yesu ataona amayi ake pamenepo ndi wophunzira amene Iye anamukonda atayima pafupipo, Iye anati kwa amayi ake, "Amayi nayu mwana wanu." 27 Anawuzanso wophunzirayo kuti, "Nawa amayi ako." Kuyambira nthawi imeneyo, wophunzirayo anatenga amayiwo kupita nawo kwawo.

Veja também

Publicidade
Bíblia Online Bíblia Online

Bíblia Online • Versão: 2026-06-29_22-07-56-