25 Pafupi ndi mtanda wa Yesu panayima amayi ake, mngʼono wa amayi ake, Mariya mkazi wa Kaliyopa ndi Mariya wa ku Magadala. 26 Yesu ataona amayi ake pamenepo ndi wophunzira amene Iye anamukonda atayima pafupipo, Iye anati kwa amayi ake, "Amayi nayu mwana wanu." 27 Anawuzanso wophunzirayo kuti, "Nawa amayi ako." Kuyambira nthawi imeneyo, wophunzirayo anatenga amayiwo kupita nawo kwawo.