Pular para o conteúdo
Publicidade

João 2

Yesu Asandutsa Madzi Kukhala Vinyo

1 Pa tsiku lachitatu munali ukwati mu Kana wa ku Galileya. Amayi ake a Yesu anali komweko, 2 ndipo Yesu ndi ophunzira ake anayitanidwanso ku ukwatiwo. 3 Vinyo atatha, amayi a Yesu anati kwa Iye, "Wawathera vinyo."

4 Yesu anayankha kuti, "Amayi, chifukwa chiyani mukundiwuza Ine? Nthawi yanga sinakwane."

5 Amayi ake anati kwa antchito, "Inu muchite chilichonse chimene akuwuzeni."

6 Pamenepo panali mitsuko yamiyala yothiramo madzi isanu ndi umodzi, imene Ayuda amagwiritsa ntchito pa mwambo wodziyeretsa. Uliwonse unali ndi malita 100 kapena kupitirirapo.

7 Yesu anati kwa antchitowo, "Dzazani madzi mʼmitsukoyi," ndipo iwo anadzaza ndendende.

8 Ndipo Iye anatinso kwa iwo, "Tsopano tungani ndipo kaperekeni kwa mkulu waphwando."

Iwo anachita momwemo. 9 Mkulu waphwando analawa madziwo amene anasandulika vinyo, ndipo sanazindikire kumene vinyoyo anachokera, ngakhale kuti antchito amene anatunga madziwo amadziwa. Kenaka anayitanira mkwati pambali 10 ndipo anati, "Aliyense amatulutsa vinyo wokoma kwambiri poyambirira ndipo kenaka vinyo wosakoma pamene oyitanidwa atamwa kale wambiri; koma iwe wasunga wokoma mpaka tsopano."

11 Ichi chinali chizindikiro chodabwitsa choyamba chimene Yesu anachita ku Kana wa ku Galileya. Potero Iye anawulula ulemerero wake, ndipo ophunzira ake anamukhulupirira Iye.

Veja também