Pular para o conteúdo
Publicidade

YOHANE 20

11 koma Mariya anayima kunja kwa manda akulira. Pamene akulira, anawerama ndi kusuzumira mʼmanda 12 ndipo anaona angelo awiri atavala zoyera, atakhala pamene panali mtembo wa Yesu, mmodzi kumutu ndi wina kumapazi.

13 Iwo anamufunsa iye kuti, "Amayi, nʼchifukwa chiyani mukulira?"

Iye anati, "Amuchotsa Mbuye wanga, ndipo ine sindikudziwa kumene iwo amuyika." 14 Atanena izi, iye anatembenuka ndipo anaona Yesu atayima potero koma iye sanazindikire kuti anali Yesu.

15 Iye anati, "Amayi, mukulira chifukwa chiyani? Ndani amene mukumufunafuna?"

Poganiza kuti anali mwini munda, iye anati, "Bwana, ngati inu mwamuchotsa, ndiwuzeni kumene mwamuyika, ndipo ine ndikamutenga."

16 Yesu anati kwa iye, "Mariya."

Anatembenukira kwa Iye nafuwula mu Chiaramaiki kuti, "Raboni!" (kutanthauza Mphunzitsi).

17 Yesu anati, "Usandigwire Ine, pakuti sindinapite kwa Atate. Mʼmalo mwake pita kwa abale anga ndikukawawuza kuti, ndikupita kwa Atate ndi kwa Atate anunso, kwa Mulungu wanga ndi Mulungu wanunso."

18 Mariya wa ku Magadala anapita kwa ophunzira ndi uthenga wakuti, "Ndamuona Ambuye!" Iye anawawuza iwo kuti Yesu ananena zinthu izi kwa iye.

Veja também