Yesu Aonekera kwa Tomasi
24 Koma Tomasi (otchedwa Didimo), mmodzi wa khumi ndi awiriwo, sanali ndi ophunzira pamene Yesu anabwera. 25 Ophunzira enawo atamuwuza Tomasi kuti iwo anaona Ambuye, iye ananenetsa kuti, "Pokhapokha nditaona zizindikiro za misomali mʼmanja ake ndi kuyikamo chala changa mʼmene munali misomali ndi kukhudza dzanja langa mʼnthiti mwake, ine sindidzakhulupirira."
26 Patapita sabata, ophunzira ake analinso mʼnyumbamo ndipo Tomasi anali nawo. Ngakhale makomo anali otsekedwa, Yesu anabwera nayima pakati pawo, ndipo anati, "Mtendere ukhale nanu!" 27 Kenaka anati kwa Tomasi, "Ika chala chako apa; ona manja anga. Tambasula dzanja lako ndi kukhudza mʼnthiti mwanga. Leka kukayika, khulupirira."
28 Tomasi anati kwa Iye, "Ambuye wanga ndi Mulungu wanga!"
29 Kenaka Yesu anamuwuza kuti, "Kodi wakhulupirira chifukwa wandiona Ine? Ndi odala amene amakhulupirira ngakhale asanaone."