3 Poyankha Yesu ananena kuti, "Zoonadi, Ine ndikukuwuza kuti, ngati munthu sabadwanso mwatsopano sangathe kuona ufumu wa Mulungu."
4 Nekodimo anati, "Kodi munthu angabadwenso bwanji atakalamba? Kodi angalowe kachiwiri mʼmimba ya amayi ake kuti abadwenso?"
5 Yesu anayankha kuti, "Zoonadi, Ine ndikukuwuza kuti ngati munthu sabadwa mwa madzi ndi Mzimu Woyera, sangalowe mu ufumu wa Mulungu. 6 Thupi limabereka thupi, koma Mzimu amabereka mzimu. 7 Iwe usadabwe chifukwa ndakuwuza kuti, ‘Uyenera kubadwanso.’ 8 Mphepo imawomba kulikonse kumene ikufuna. Ungathe kumva kuwomba kwake, koma sungathe kudziwa kumene ikuchokera kapena kumene ikupita. Nʼchimodzimodzi ndi amene abadwa ndi Mzimu Woyera."