19 Mayiyo anati, "Ambuye, ine ndazindikira kuti Inu ndinu mneneri. 20 Makolo athu ankapembedza mʼphiri ili koma inu Ayuda mumati malo amene tiyenera kupembedzera ali ku Yerusalemu."
21 Yesu anati, "Mayi inu khulupirira Ine. Nthawi ikubwera pamene inu simudzapembedza Atate mʼphiri ili kapena mu Yerusalemu. 22 Inu Asamariya mumapembedza chimene simukuchidziwa. Ife timapembedza chimene tikuchidziwa, pakuti chipulumutso nʼchochokera kwa Ayuda. 23 Koma nthawi ikubwera ndipo yafika kale tsopano pamene opembedza woona adzapembedza Atate mu mzimu ndi mʼchoonadi, pakuti opembedza otere ndiwo amene Atate akuwafuna. 24 Mulungu ndi Mzimu, ndipo omupembedza Iye ayenera kumupembedza mu mzimu ndi mʼchoonadi."
25 Mayiyo anati, "Ine ndikudziwa kuti Mesiya (wotchedwa Khristu) akubwera. Akabwera, Iye adzafotokoza zonse kwa ife."
26 Ndipo Yesu anamuwuza kuti, "Amene ndikukuyankhulane, ndine amene."