21 Yesu anati, "Mayi inu khulupirira Ine. Nthawi ikubwera pamene inu simudzapembedza Atate mʼphiri ili kapena mu Yerusalemu. 22 Inu Asamariya mumapembedza chimene simukuchidziwa. Ife timapembedza chimene tikuchidziwa, pakuti chipulumutso nʼchochokera kwa Ayuda. 23 Koma nthawi ikubwera ndipo yafika kale tsopano pamene opembedza woona adzapembedza Atate mu mzimu ndi mʼchoonadi, pakuti opembedza otere ndiwo amene Atate akuwafuna.