31 Pa nthawi imeneyi ndi kuti ophunzira ake akumukakamiza kuti, "Rabi idyani."
32 Koma Iye anawawuza kuti, "Ine ndili ndi chakudya choti ndidye chimene inu simukuchidziwa."
33 Ndipo ophunzira ake anafunsana wina ndi mnzake kuti, "Kodi alipo wina amene anamubweretsera Iye chakudya?"
34 Yesu anati, "Chakudya changa ndikuchita chifuniro cha Iye amene anandituma Ine ndi kumaliza ntchito yake.