Pular para o conteúdo
Publicidade

João 4

46 Iye anakafikanso ku Kana wa ku Galileya, kumene anasanduliza madzi kukhala vinyo. Ndipo kumeneko kunali nduna ina ya mfumu imene mwana wake wamwamuna anali chigonere akudwala ku Kaperenawo. 47 Munthu uyu atamva kuti Yesu wafika ku Galileya kuchokera ku Yudeya, anapita kwa Iye, namupempha kuti apite akachiritse mwana wakeyo, amene anali pafupi kufa.

48 Yesu anawawuza iwo kuti, "Anthu inu pokhapokha mutaona zizindikiro zodabwitsa, simudzakhulupirira."

49 Nduna ya mfumuyo inati, "Ambuye tiyeni mwana wanga asanafe."

50 Yesu anayankha kuti, "Pita. Mwana wako adzakhala ndi moyo."

Munthuyo anakhulupirira mawu a Yesu ndipo ananyamuka. 51 Iye ali pa njira, antchito ake anakumana naye, namuwuza kuti mwana wanu uja wachira. 52 Iye atafunsa kuti ndi nthawi yanji imene mwana wake anapeza bwino, iwo anati kwa iye, "Malungo anamusiya iye dzulo pa ora lachisanu ndi chiwiri."

53 Ndipo bamboyo anazindikira kuti iyi inali nthawi yomweyo imene Yesu anati kwa iye, "Mwana wako adzakhala ndi moyo." Choncho iye ndi onse a pa banja lake anakhulupirira.

54 Ichi ndiye chinali chizindikiro chodabwitsa chachiwiri chimene Yesu anachita atafika ku Galileya kuchokera ku Yudeya.

Veja também