Pular para o conteúdo
Publicidade

João 5

Yesu Achiritsa Munthu pa Sabata

1 Patapita nthawi Yesu anakwera kupita ku Yerusalemu ku phwando la Ayuda. 2 Ndipo ku Yerusalemuko pafupi ndi chipata cha Nkhosa kuli dziwe limene mʼChihebri limatchedwa Betisaida ndipo ndi lozunguliridwa ndi makumbi asanu. 3 Mʼmenemo munkagonamo gulu lalikulu la anthu odwala, osaona, olumala ndi ofa ziwalo. 4 Pakuti nthawi zina mngelo wa Ambuye ankatsikira mʼdziwemo nʼkuvundula madziwo. Woyamba kulowamo madzi atavundulidwa, ankachira ngakhale akhale ndi nthenda yanji. 5 Mmodzi wa amene anali pamenepo anali atadwala zaka 38. 6 Yesu atamuona ali chigonere, nadziwa kuti anakhala chotero kwa nthawi yayitali, anamufunsa iye kuti, "Kodi ukufuna kuchira?"

7 Wodwalayo anayankha kuti, "Ambuye, ndilibe wina aliyense woti angandithandize kulowa mʼdziwe pamene madzi avundulidwa. Pamene ndikuyesera kuti ndilowemo, wina amalowamo ine ndisanalowemo."

8 Ndipo Yesu anati kwa iye, "Imirira! Nyamula mphasa yako yamba kuyenda." 9 Nthawi yomweyo munthuyo anachiritsidwa. Iye ananyamula mphasa yake nayamba kuyenda.

Tsiku limene izi zinachitika linali la Sabata.

Veja também