Pular para o conteúdo
Publicidade

João 6

Yesu Adyetsa Anthu 5,000

1 Nthawi ina zitatha izi, Yesu anawolokera ku gombe la kutali la nyanja ya Galileya (iyi ndi nyanja ya Tiberiya), 2 ndipo gulu lalikulu la anthu linamutsata Iye chifukwa linaona zizindikiro zodabwitsa zimene anazichita pa odwala. 3 Kenaka Yesu anakwera pa phiri nakhala pansi ndi ophunzira ake. 4 Tsopano phwando la Paska la Ayuda linali pafupi.

5 Yesu atakweza maso ndi kuona gulu lalikulu la anthu likubwera kwa Iye, anati kwa Filipo, "Kodi tingagule kuti buledi kuti anthu awa adye?" 6 Iye anafunsa izi kumuyesa chabe, pakuti Iye ankadziwa chimene ankayenera kuchita.

7 Filipo anamuyankha Iye kuti, "Malipiro a miyezi isanu ndi itatu sangathe kugula buledi okwanira aliyense kuti adye!"

8 Mmodzi wa ophunzira ake, Andreya, mʼbale wa Simoni Petro, anati, 9 "Pano pali mnyamata amene ali ndi buledi musanu wabarele ndi tinsomba tiwiri, kodi zingakwane onsewa?"

10 Yesu anati, "Awuzeni anthuwa akhale pansi." Pamalo pamenepa panali udzu wambiri ndipo amuna amene anakhala pansi anali osachepera 5,000. 11 Kenaka Yesu anatenga bulediyo, atayamika anagawira iwo amene anakhala pansi, chimodzimodzinso nsombazo monga momwe iwo anafunira.

12 Ndipo atakhuta, Iye anati kwa ophunzira ake, "Tolani zotsala kuti pasawonongeke kanthu." 13 Choncho iwo anasonkhanitsa makombo nadzaza madengu khumi ndi awiri.

14 Pambuyo pake anthu ataona chizindikiro chodabwitsa chimene Yesu anachita, iwo anati, "Zoonadi uyu ndi Mneneri wakudzayo mʼdziko la pansi."

Veja também