Pular para o conteúdo
Publicidade

João 6

32 Yesu anawawuza kuti, "Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti si Mose amene ankakupatsani chakudya chochokera kumwamba, koma ndi Atate anga amene ankakupatsani chakudya chenicheni chochokera kumwamba. 33 Pakuti chakudya cha Mulungu ndi Iye amene wabwera kuchokera kumwamba ndi kupereka moyo ku dziko la pansi."

34 Iwo anati, "Ambuye, kuyambira tsopano muzitipatsa buledi ameneyu."

35 Kenaka Yesu ananenetsa kuti, "Ine ndine chakudya chamoyo. Iye amene abwera kwa Ine sadzamva njala, ndipo iye amene akhulupirira Ine sadzamva ludzu.

Veja também