Publicidade

João 6

53 Yesu anawawuza kuti, "Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti ngati simungadye thupi la Mwana wa Munthu ndi kumwa magazi ake, simungakhale ndi moyo mwa inu. 54 Aliyense amene adya thupi langa ndi kumwa magazi anga ali ndi moyo wosatha ndipo Ine ndidzamuukitsa kwa akufa pa tsiku lomaliza. 55 Pakuti thupi langa ndi chakudya chenicheni ndipo magazi anga ndi chakumwa chenicheni. 56 Aliyense amene adya thupi langa ndi kumwa magazi anga amakhala mwa Ine, ndi Ine mwa iye. 57 Monga Atate amoyo anandituma Ine, ndipo ndili ndi moyo chifukwa cha Atatewo, chomwechonso amene adya thupi langa adzakhala ndi moyo chifukwa cha Ine. 58 Ichi ndiye chakudya chimene chinatsika kuchokera kumwamba. Makolo athu akale anadya mana ndi kufa, koma iye amene adya chakudya ichi, adzakhala ndi moyo nthawi yonse."

Veja também

Bíblia Online Bíblia Online

Bíblia Online • Versão: 2026-07-05_19-25-13-