6 Iye anafunsa izi kumuyesa chabe, pakuti Iye ankadziwa chimene ankayenera kuchita.
7 Filipo anamuyankha Iye kuti, "Malipiro a miyezi isanu ndi itatu sangathe kugula buledi okwanira aliyense kuti adye!"
8 Mmodzi wa ophunzira ake, Andreya, mʼbale wa Simoni Petro, anati, 9 "Pano pali mnyamata amene ali ndi buledi musanu wabarele ndi tinsomba tiwiri, kodi zingakwane onsewa?"
10 Yesu anati, "Awuzeni anthuwa akhale pansi." Pamalo pamenepa panali udzu wambiri ndipo amuna amene anakhala pansi anali osachepera 5,000. 11 Kenaka Yesu anatenga bulediyo, atayamika anagawira iwo amene anakhala pansi, chimodzimodzinso nsombazo monga momwe iwo anafunira.
12 Ndipo atakhuta, Iye anati kwa ophunzira ake, "Tolani zotsala kuti pasawonongeke kanthu." 13 Choncho iwo anasonkhanitsa makombo nadzaza madengu khumi ndi awiri.