66 Kuyambira nthawi imeneyi ophunzira ake ambiri anabwerera ndipo sanamutsatenso Iye.
67 Yesu anafunsa khumi ndi awiriwo kuti, "Kodi inu mukufuna kuchokanso?"
68 Simoni Petro anamuyankha Iye kuti, "Ambuye, ife tidzapita kwa yani? Inu muli ndi mawu amoyo wosatha. 69 Ife tikhulupirira ndi kudziwa kuti Inu ndinu Woyerayo wa Mulungu."