Publicidade

João 7

Yesu Aphunzitsa pa Phwando

14 Phwando lili pakatikati, Yesu anapita ku bwalo la Nyumba ya Mulungu ndi kuyamba kuphunzitsa. 15 Ayuda anadabwa ndipo anafunsa kuti, "Kodi munthu uyu nzeru izi anazitenga kuti popanda kuphunzira?"

16 Yesu anayankha kuti, "Chiphunzitso changa si cha Ine ndekha. Chimachokera kwa Iye amene anandituma. 17 Ngati munthu asankha kuchita chifuniro cha Mulungu, adzazindikira ngati chiphunzitso changa nʼchochokera kwa Mulungu kapena ngati ndi mwa Ine ndekha. 18 Iye amene amayankhula za Iye mwini amatero kuti adzipezere ulemu, koma amene amagwira ntchito kuti amene anamutuma alandire ulemu, ameneyo ndiye munthu woona; mu mtima mwake mulibe chinyengo chilichonse.

Veja também

Publicidade
Bíblia Online Bíblia Online

Bíblia Online • Versão: 2026-06-28_14-13-17-