4 anati kwa Yesu, "Aphunzitsi, mkazi uyu tinamugwira akuchita chigololo. 5 Mʼmalamulo a Mose anatilamulira kuti akazi otere tiwagende ndi miyala. Tsopano Inu mukuti chiyani?" 6 Iwo anagwiritsa ntchito funsoli ngati msampha, ndi cholinga choti apeze chifukwa cha kumuneneza Iye.
Koma Yesu anawerama pansi ndi kuyamba kulemba pa dothi ndi chala chake. 7 Pamene iwo anapitirira kumufunsa, Iye anaweramuka ndipo anawawuza kuti, "Ngati wina wa inu alipo wopanda tchimo, ayambe iyeyo kumugenda ndi miyala mkaziyu." 8 Iye anaweramanso pansi ndi kulemba pa dothi.
9 Iwo atamva izi anayamba kuchoka mmodzimmodzi, akuluakulu poyamba, mpaka Yesu anatsala yekha ndi mkaziyo atayimirira pomwepo. 10 Yesu anaweramuka ndipo anamufunsa iye kuti, "Akuluakulu aja ali kuti? Kodi palibe amene wakutsutsa?"
11 Iye anati, "Ambuye, palibe ndi mmodzi yemwe."
"Inenso sindikukutsutsa iwe. Pita kuyambira tsopano usakachimwenso."