Yesu Achiritsa Munthu Wosaona Chibadwire
1 Iye akuyendabe, anaona munthu wosaona chibadwire. 2 Ophunzira ake anamufunsa Iye kuti, "Rabi anachimwa ndani, munthuyu kapena makolo ake, kuti iye abadwe wosaona?"
3 Yesu anayankha kuti, "Sikuti iyeyu anachimwa kapena makolo ake, koma izi zinachitika kuti Mulungu aonetse ntchito zake mwa iyeyu. 4 Ife tiyenera kugwira ntchito za Iye amene anandituma kukanali masana. Usiku ukubwera, pamene wina aliyense sadzagwira ntchito. 5 Pamene Ine ndili mʼdziko lapansi, Ine ndine kuwunika kwa dziko lapansi."
6 Atanena izi, Iye anathira malovu pansi ndi kukanda dothi, napaka matopewo mʼmaso a munthuyo. 7 Yesu anamuwuza iye kuti, "Pita kasambe mʼdziwe la Siloamu" (mawu awa akutanthauza Wotumidwa). Choncho munthuyo anapita ndi kukasamba ndipo anabwerako akupenya.
8 Anzake ndi iwo amene anamuona iye poyamba akupempha anafunsa kuti, "Kodi uyu si munthu amene amapemphapempha uja?" 9 Ena ananena kuti anali yemweyo.
Ena anati, "Ayi, sakuoneka ngati yemweyo."
Koma iye mwini ananenetsa kuti, "Munthuyo ndine."
10 Iwo anafunsitsa kuti, "Kodi nanga maso ako anatsekuka bwanji?"
11 Iye anayankha kuti, "Munthu wina wotchedwa Yesu anakanda dothi ndi kupaka mʼmaso anga. Iye anandiwuza kuti ndipite ku Siloamu ndi kukasamba. Choncho ndinapita kukasamba, ndipo ndikuona."
12 Iwo anamufunsa iye kuti, "Ali kuti munthu ameneyu?"
Iye anati, "Ine sindikudziwa."