Yesu Achiritsa Munthu Wosaona Chibadwire
1 Iye akuyendabe, anaona munthu wosaona chibadwire. 2 Ophunzira ake anamufunsa Iye kuti, "Rabi anachimwa ndani, munthuyu kapena makolo ake, kuti iye abadwe wosaona?"
3 Yesu anayankha kuti, "Sikuti iyeyu anachimwa kapena makolo ake, koma izi zinachitika kuti Mulungu aonetse ntchito zake mwa iyeyu. 4 Ife tiyenera kugwira ntchito za Iye amene anandituma kukanali masana. Usiku ukubwera, pamene wina aliyense sadzagwira ntchito. 5 Pamene Ine ndili mʼdziko lapansi, Ine ndine kuwunika kwa dziko lapansi."
6 Atanena izi, Iye anathira malovu pansi ndi kukanda dothi, napaka matopewo mʼmaso a munthuyo. 7 Yesu anamuwuza iye kuti, "Pita kasambe mʼdziwe la Siloamu" (mawu awa akutanthauza Wotumidwa). Choncho munthuyo anapita ndi kukasamba ndipo anabwerako akupenya.