30 Yefita analumbira kwa Yehova kuti, "Ngati mupereka Aamoni mʼmanja mwanga, 31 aliyense amene atuluke pa khomo la nyumba yanga kudzandichingamira pobwerera nditagonjetsa Aamoni adzakhala wake wa Yehova, ndipo ndidzamupereka kuti akhale nsembe yopsereza."