34 Pambuyo pake Yefita anabwerera ku nyumba yake. Tsono anangoona mwana wake wamkazi akutuluka kudzamuchingamira akuyimba ngʼoma ndi kuvina. Uyu anali mwana yekhayo wa Yefita. Analibenso mwana wina wamwamuna kapena wamkazi. 35 Yefita ataona mwana wake uja, anangʼamba zovala zake ndi kulira, "Kalanga ine! Mwana wanga! Wandivulaza kwambiri ndipo iwe ndi gwero la mavuto anga. Ine ndinalumbira kwa Yehova ndi pakamwa pangapa ndipo sindingathe kubweza malumbiro angawo."