Publicidade

Lucas 1

34 Mariya anafunsa mngeloyo kuti, "Izi zingatheke bwanji popeza ine sindidziwa mwamuna?"

35 Mngelo anayankha kuti, "Mzimu Woyera adzabwera pa iwe ndipo mphamvu ya Wammwambamwamba idzakuphimba, ndipo Woyerayo amene adzabadwe adzatchedwa Mwana wa Mulungu. 36 Ngakhale Elizabeti mʼbale wako adzakhala ndi mwana mu ukalamba wake ndipo iye amene amati ndi wosabereka, uno mwezi wake wachisanu ndi chimodzi. 37 Pakuti palibe chinthu chosatheka ndi Mulungu."

38 Mariya anayankha kuti, "Ine ndine mtumiki wa Ambuye. Zikhale kwa ine monga mwanenera."

Veja também

Bíblia Online Bíblia Online

Bíblia Online • Versão: 2026-07-04_21-26-40-