59 Pa tsiku lachisanu ndi chitatu anabwera ndi mwana kuti adzachitidwe mdulidwe, ndipo anafuna kumupatsa dzina la abambo ake Zakariya, 60 koma amayi ake anayankhula nati, "Ayi, atchulidwe kuti Yohane."
61 Iwo anati kwa iye, "Palibe mmodzi mwa abale ake amene ali ndi dzina limeneli."
62 Pamenepo anapanga zizindikiro kwa abambo ake kuti adziwe dzina limene akanakonda kumutcha mwanayo. 63 Iye anapempha poti alembepo, ndipo chodabwitsa kwa aliyense analemba kuti, "Dzina lake ndi Yohane." 64 Nthawi yomweyo pakamwa pake panatsekuka ndi lilime lake linamasuka ndipo anayamba kuyankhula, nayamika Mulungu.