Pular para o conteúdo
Publicidade

Lucas 1

Nyimbo ya Zakariya

67 Abambo ake, Zakariya, anadzazidwa ndi Mzimu Woyera ndipo ananenera kuti,

68 "Alemekezeke Ambuye, Mulungu wa Israeli

chifukwa wabwera ndi kuwombola anthu ake.

69 Iye wakweza nyanga yachipulumutso kwa ife

mu nyumba ya mtumiki wake Davide.

70 (Monga mmene ananenera kudzera mwa aneneri oyera),

71 chipulumutso kuchoka kwa adani athu

ndi kuchoka mʼdzanja la onse otida,

72 kuonetsa chifundo kwa makolo athu

ndi kukumbukira pangano lake loyera,

73 lumbiro limene analumbira kwa kholo lathu Abrahamu:

74 kutilanditsa ife mʼdzanja la adani athu,

ndi kutipanga ife timutumikire Iye mopanda mantha,

75 mʼchiyero ndi mʼchilungamo masiku athu onse.

76 "Ndipo iwe mwana wanga udzatchedwa mneneri wa Wammwambamwamba;

pakuti udzapita patsogolo pa Ambuye kukonza njira yake,

77 kupatsa anthu ake chidziwitso cha chipulumutso

kudzera mwa chikhululukiro cha machimo awo,

78 chifukwa cha chifundo chachikulu cha Mulungu wathu,

ndipo kuwala kwa dzuwa kudzafikira ife kuchokera kumwamba,

79 kuwalira iwo okhala mu mdima

ndi mu mthunzi wa imfa,

kutsogolera mapazi athu mu njira yamtendere."

Veja também