Fanizo la Msamariya Wachifundo
25 Nthawi ina katswiri wa malamulo anayimirira kuti ayese Yesu. Iye anati, "Aphunzitsi, ndichite chiyani kuti ndikhale ndi moyo wosatha?"
26 Yesu anayankha kuti, "Mwalembedwa chiyani mʼMalamulo, ndipo iwe umawerenga zotani?"
27 Iye anayankha kuti, "Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi mphamvu zako zonse ndi nzeru zako zonse, ndi kukonda mnansi wako monga iwe mwini."
28 Yesu anayankha kuti, "Iwe wayankha bwino, chita zimenezi ndipo udzakhala ndi moyo."