15 Kenaka Iye anawawuza kuti, "Chenjerani! Khalani tcheru ndi makhalidwe onse adyera; moyo wa munthu sukhala chifukwa cha kuchuluka kwa zimene ali nazo."
16 Ndipo Iye anawawuza fanizo ili, "Munda wa munthu wina wachuma unabereka kwambiri. 17 Iye anaganiza kuti, ‘Ndichite chiyani? Ndilibe malo osungiramo mbewu zanga.’
18 "Ndipo Iye anati, ichi ndi chimene ndidzachite: Ndidzaphwasula nkhokwe zanga zonse ndi kumanga zokulirapo, ndipo ndidzasungira mʼmenemo mbewu ndi katundu. 19 Ndipo ndidzawuza moyo wanga kuti, ‘Uli nazo zinthu zabwino zambiri zimene zikhalepo zaka zambiri, usapupulume; idya, imwa ndi kukondwera.’ "
20 "Koma Mulungu anati kwa iye, ‘Iwe wopusa! Usiku womwe uno moyo wako udzachotsedwa kwa iwe, ndipo ndi ndani amene adzatenge zimene iwe wadzikonzera?’
21 "Umu ndi mmene zidzakhalire ndi aliyense amene amadziwunjikira chuma, koma si wachuma pamaso pa Mulungu."