Pular para o conteúdo
Publicidade

Lucas 14

Yesu Mʼnyumba ya Mfarisi

1 Pa tsiku lina la Sabata, Yesu atapita kukadya ku nyumba ya Mfarisi wodziwika, Afarisi anamulonda mosamalitsa. 2 Poteropo, patsogolo pake panali munthu amene anadwala matenda otupa mimba ndi miyendo. 3 Yesu anafunsa Afarisi ndi akatswiri amalamulo kuti, "Kodi ndi zololedwa kuchiritsa pa tsiku la Sabata kapena ayi?" 4 Koma iwo sanayankhe. Tsono atamutenga munthuyo, Iye anamuchiritsa ndipo anamuwuza kuti azipita.

Veja também