Fanizo la Nkhosa Yotayika
1 Tsopano amisonkho ndi "ochimwa" ankasonkhana kudzamvera mawu ake. 2 Koma Afarisi ndi aphunzitsi amalamulo amangʼungʼudza nati, "Munthu uyu amalandira ochimwa ndi kudya nawo."
3 Ndipo Yesu anawawuza fanizo ili: 4 "Tiyerekeze kuti mmodzi mwa inu ali ndi nkhosa 100 ndipo imodzi yatayika, kodi iye sangasiye 99 zija kutchire ndi kupita kukafuna yotayikayo mpaka atayipeza? 5 Ndipo iye akayipeza, amayinyamula pa phewa lake mwachimwemwe 6 ndi kupita kwawo. Kenaka amayitana anzake ndi anansi pamodzi, ndi kuti, ‘Kondwerani nane; ine ndayipeza nkhosa yanga yotayika ija.’ 7 Ine ndikukuwuzani kuti momwemonso kudzakhala chikondwerero chachikulu kumwamba chifukwa cha wochimwa mmodzi amene watembenuka mtima kusiyana ndi anthu olungama 99 amene ali otembenuka mtima kale."