Fanizo la Mwana Wolowerera
11 Yesu anapitiriza kunena kuti, "Panali munthu amene anali ndi ana aamuna awiri. 12 Wamngʼonoyo anati kwa abambo ake, ‘Abambo, patseni gawo langa la chuma chanu.’ Ndipo iye anawagawira awiriwo chuma chawo.
13 "Pasanapite nthawi, wamngʼonoyo anasonkhanitsa chuma chake chonse, napita ku dziko lakutali ndipo kumeneko anayamba kumwaza chuma chake mʼnjira zachitayiko.
20 Ndipo iye ananyamuka ndi kupita kwa abambo ake.
"Koma iye akanali patali, abambo ake anamuona ndipo anamvera chisoni; anathamangira mwanayo, namukumbatira ndi kupsompsona.
22 "Koma abambowo anati kwa antchito ake, ‘Fulumirani! Bweretsani mkanjo wabwino kwambiri ndipo mumuveke. Muvekeni mphete ndi nsapato. 24 Pakuti mwana wangayu anali wakufa, ndipo ali ndi moyonso; iye anatayika ndipo wapezeka.’ Chomwecho anayamba kukondwerera.