Pular para o conteúdo
Publicidade

Luka 15:11-13,20,22,24

NTNYBL2025 Nyanja

Chifani cha mnyamata wataika

11 Pamenepo Yesu wadayendekela kukamba, "Kudali mundhu mmoji uyo wadali ni anyamata awili waachimuna. 12 Wamng’ono wadaakambila atate wake, ‘Atate, munipache vilanjo vanga.’ Ndiipo atate wao adagawa vindhu vao ni kumpacha chuma chake mwana wamng’onoyo. 13 Pambuyo pa masiku yochepa, mwana wamng’ono yujha wadatenga chuma chonjhe ni kupita ku jhiko la kutali, kumeneko wadatumila chuma chake kwa kuwananga. 20 Ndiipo wadayamba ulendo wopita kwa atate wake. Nambho yapo wadali wakali patali, atate wake adamuona, adamlengela lisungu. Adamthamangila mwana wao ni kumkhumbatila kwa chisangalalo. 22 Nambho atate wake adaakambila mbowa zake, ‘Pita chisanga katenge njhalu yabwino mumveke! Mvekeni pete ni malapasi ya mtengo waukulu! 24 Chifuko mwanawangayu wadamwalila, nambho chipano wali wamoyo, wadataika, nambho wapatikana.’ Ndiipo adayamba kuchita phwando."

Em outras traduções

  1. TCCL Abra a Palavra de Deus em Chichewa Contemporâneo

    11 Yesu anapitiriza kunena kuti, "Panali munthu amene anali ndi ana aamuna awiri. 12 Wamngʼonoyo anati kwa abambo ake, ‘Abambo, patseni gawo langa la chuma chanu.’ Ndipo iye anawagawira awiriwo chuma chawo.

    13 "Pasanapite nthawi, wamngʼonoyo anasonkhanitsa chuma chake chonse, napita ku dziko lakutali ndipo kumeneko anayamba kumwaza chuma chake mʼnjira zachitayiko.

    20 Ndipo iye ananyamuka ndi kupita kwa abambo ake.

    "Koma iye akanali patali, abambo ake anamuona ndipo anamvera chisoni; anathamangira mwanayo, namukumbatira ndi kupsompsona.

    22 "Koma abambowo anati kwa antchito ake, ‘Fulumirani! Bweretsani mkanjo wabwino kwambiri ndipo mumuveke. Muvekeni mphete ndi nsapato. 24 Pakuti mwana wangayu anali wakufa, ndipo ali ndi moyonso; iye anatayika ndipo wapezeka.’ Chomwecho anayamba kukondwerera.

Direitos das traduções citadas

Estes versículos te tocaram? Ore agora!

+581 estão orando agora.

Junte-se à corrente de oração.