1 Masiku yameneyo Agusito mfumu wa kuloma wadachocha lamulo lakuti wandhu wonjhe apajhiko la kuloma awelengedwe. 2 Kuwelengedwa kumeneko kudali koyamba yapo Kilenio wadali wamkulu wa jhiko la Siliya. 3 Ndiipo kila mundhu wadapita kukawelengedwa kumujhi kwake uko wadabadwila.
4 Yusufu wadachoka kumujhi wa ku Nazaleti uwo uli mujhiko la ku galilaya, wadapita kumujhi wa Beselehemu uwo uli kujhiko la Yudea, uko wadabadwila mfumu Daudi. Yusufu wadapita kumeneko ndande iye wadali wa mbadwa wa mfumu Daudi. 5 Iye wadapita kuwelengedwa pamojhi ni Maliya, uyo wadampacha chilipa, nayo wadali ni pathupi. 6 Yapo adali kumeneko ku Beselehemu, ndhawi yojhipenyelela Maliya idakwanila, 7 ni wadajhimasula mwana wake wachisamba, wammuna. Iye wadamvinikila matewela ni kumgoneka mchidiku chasependwa ndande yodyechela ng'ombe, chifuko anyiiwo siadapate malo mnyumba ya alendo.
8 Ni pamalo pamenepo padali ni owesa amakhala pafupi ni pamenepo amalonda mbelele zao ndhawi ya usiku. 9 Mtumiki wa kumwamba wa Mnungu wadatulukila mwachizulumukila, ni dangalila la ulemelelo wa Ambuye lidawalila njhonga zonjhe. Nianyiiwo adaopa kupunda. 10 Nambho mtumiki wa kumwamba wa Mnungu wadaakambila, "Msadaopa! Nakupelekelani uthenga wabwino uwo siwakondweleche kupunda wandhu wonjhe. 11 Pakuti lelo mmujhi wa Daudi wabadwa olamicha ndande yanu, iye nde Kilisito Ambuye. 12 Ichi nde chizindikilo chanu, simumkomane mwana wakhanda uyo wavekedwa matewela ni wagonekedwa mchidiku cho dyechela ng'ombe." 13 Mwachizulumukila gulu la lalikulu la atumiki akumwamba lidatulukila lili pamojhi ni achanjao atumiki wa kumwamba wa Mnungu, niamtamanda Mnungu niakamba,
14 "Ulemelelo ukhale kwa Mnungu wali kumwamba kupunda
ni pano pajhiko lapanjhi pakhale ni mtendele
kwa wandhu yawo waakonda!"
15 Yapo atumiki akumwamba a Mnungu adaasiya ni kupita kumwamba, owesa wajha adakambilana, adakamba, "Tiyeni ku Beselehemu tikaone icho chachokela, icho takambilidwa ni Ambuye."
16 Chimwecho, adapita msangamsanga ni kumkomana Maliya ni Yusufu, ni mwana wakhanda, uyo wadagonekedwa mchidiku cha sepedwa ndande yo dyechela Ng'ombe. 17 Owesa wajha yapo adamuona mwanayo, adauzila wandhu wina nghani za mwana mmeneyo izo adakambilidwa ni atumiki akumwamba kuhusu mwana. 18 Ni wandhu wonjhe yawo adavela nghani za mwana zo amakamba owesa zinyama adazizwa kupunda. 19 Nambho Maliya wadaganizila ni kuyasunga mawu yajha mumtima mwake. 20 Ndiipo owesa zinyama wajha adabwelela kuphululu uku namtamanda ni kumkweza Mnungu ndande ya yayo adayavela ni kuyaona ngati umo adakambidwila.
21 Yapo lidafika Siku la nane, mwana wadadulidwa jhando, ni kumpacha jhina Yesu, jhina ilo wadapachidwa ni mtumiki wa kumwamba wa Mnungu yapo Maliya wakali osapate pathupi.
22 Masiku yosamba naye mwana yapo yadakwana, ngati umo lidali thauko la Mnungu ilo wadampacha Musa, anyakubala wake adamtenga mwana ni kupitanayo ku Yelusalemu kuti akampeleke pamaso pa Ambuye. 23 Ngati umo idalembedwela mu thauko la Ambuye kuti, "Kila mwana wammuna wachisamba siwapatulidwe ndande ya Ambuye." 24 Naonjho adapita kuti akachoche mahoka kwa Mnungu, maliunda yawili ya nghunda ngati lifunikila thauko la Ambuye.
25 Nyengo imeneyo kudali mundhu mmojhi mu Yelusalemu uyo wamatanidwa Simiyoni, wadali wovomelezeka ni woopa Mnungu. Iye wamalindilila kujha kwa uomboli wa Izilaeli, ni Mzimu Woyela udali ni iye. 26 Mzimu Woyela udamchimikizila kuti siwafa mbaka yapo siwamuone Kilisito uyo wasanghidwa ni Ambuye. 27 Ndiipo Mzimu wa Mnungu udamchogoza Simiyoni kulowa pa Nyumba ya Mnungu. Anyakubala a Yesu adampeleka mwana wao pa Nyumba ya Mnungu kuti amuchite ngati umo lifunila khalidwe, 28 Simiyoni wadamtenga mwana yujha mmanja mwake uku niwamtamanda Mnungu, pokamba,
29 "Chipano Ambuye mwakwanilicha ahadi zanu,
munilole mbowa wanu nimwalile kwa mtendele.
30 Pakuti nauona uomboli wanu kwa maso yanga,
31 uwo mwaupeleka kuti uonekane kwa wandhu amaiko yonjhe.
32 Dangalila la kwawalila wandhu yawo osati Ayahudi,
ni ukulu kwa wandhu wanu ajhiko la Izilaeli."
33 Atate wake ni amake a Yesu amangozizwa mawu yonjhe yayo yamakambidwa yakuusu mwana. 34 Simiyoni wadaapacha mwawi, ni kumkambila Maliya make wa mwana, "Mwana uyu siwakhale chifuko cha khugwa ni kuomboka wandhu ambili mu Izilaeli. Iye siwakhale chizindikilo chochokela kwa Mnungu icho sichikanidwe ni wandhu ambili, 35 ni maganizo ya wandhu ambili siyaonekane padanga, ni iwe umwene wake siudandaule kupunda."
36 Kudali wamkazi mmojhi mlosi wamatanidwa Ana, mwana wamkazi wa Fanueli, wafuko la Asheli wadali mzee kupunda. Pa umwali wake wadakwatiwa ni kukhala ni mmunake kwa vyaka saba, ndiipo mmunake wadamwalila. 37 Chimwecho, wadakhala wafedwa ni mmunake mbaka yapo wadali ni vyaka semanini ni vinayi. Ndhawi yonjheyi wamakhala pa Nyumba ya Mnungu nambho wamamlambila Mnungu usiku ni usana popande kudya ni wapembhela. 38 Ndhawi imweyo Ana wadatulukila pachogolo pa Yusufu ni Maliya, wadamuyamika Mnungu, ni kukamba nghani za mwanayo kwa wandhu wonjhe yawo amalindilila uomboli wa ku Yelusalemu.
39 Yusufu ni Maliya yapoadamaliza kuchita yonjhe yayo yadalamulidwa ni thauko la Ambuye Mnungu, adabwela kwao ku Nazaleti ya mujhi wa Galilaya. 40 Mwana yujha wadayendekela kukula ni kukhala wanghongono, wadajhala hekima, ni ubwino wa Mnungu udali ni iye.
41 Yusufu ni Maliya adali ni chikalidwe chopita ku Yelusalemu kila chaka ndhawi ya phwando la Pasaka. 42 Yapo Yesu wadafika msinghu wa vyaka khumi ni viwili, wadapita pamojhi ni wobala wake kuphwando ngati umo chidali chikalidwe chao. 43 Yapo lidatha phwando lijha, wobala wake adayamba ulendo wobwelela kupita ku Yelusalemu, nambho Yesu wadakhalila ku Yelusalemu popande kujhiwa wobala wake. 44 Anyaiwo amaganiza kuti wali pamojhi ni gulu la ulendo, chimwecho adayenda siku lambhumbhu. Ndiipo adayamba kumfunafuna pakati pa abale ni abwenji. 45 Yapo adalepela kumuona, adabwelela ku Yelusalemu kumfunafuna.
46 Pambuyo pa masiku yatatu adamuona panyumba ya Mnungu, wakhala pakatikati pa oyaluza thauko, niwavechela ni kwaafunjha mafunjho. 47 Wandhu wonjhe adavela mayaluzo yake adazizwa kujhiwa kwake ni umo wamayanghila kwa hekima. 48 Wobala wake yapo adamuona adazizwa kupunda. Maliya, make wamwanayo wadamfunjha, "Mwana wanga, ndande yanji watichitila chimwechi? Atate wako ni ine timakufunafuna tali ni mandha." 49 Iye wadaafunjha, "Ndande yanji mnifunafuna ine? Bwanji, simujhiwa kuti ine nifunika kukhalapo panyumba ya atate wanga?" 50 Nambho wobala wake siadajhiwe mate ya mawu yayo wadakambila mwana wao.
51 Ndiipo Yesu wadabwela pamojhi ni anyiiwo mbaka ku Nazaleti, iye wamavela. Nambho amake adavisunga vindhu vonjhe mumtima. 52 Nayo Yesu wadaendekela kukula msinghu ni hekima, wadayendekela kumkhadwilicha Mnungu ni wandhu.