Publicidade

Lucas 11

Yesu wayaluza oyaluzidwa wake mtundu wopembhela

1 Siku limojhi Yesu wamapembhela kumalo fulani. Yapo wadamaliza kupembhela, mmojhi wa oyaluzidwa wake wadamkambila, "Ambuye, tikupembhani mutiyaluze kupembhela ngati umo Yohana Mbatizi wadayaluzila oyaluzidwa wake." 2 Yesu wadakambila, "Yapo mupembhela, kambani chimwechi,

‘Atate wathu akumwamba!

Jhina lanu lilemekezedwe kuti ni Loyela,

ufumu wanu ujhe.

3 Mutipache chakudya chathu cha siku ni siku.

4 Mutilekelele volakwa vathu,

ngati umo ife talekelela yawo atilakwila,

musaditipeleka mmayeselo.’ "

5 Ndiipo Yesu wadakambila, "Tikambe mmojhi wanu wali ni bwenji, wamujhela pakati pa usiku ni kumkambila, ‘Bwenji langa, nikongole mabumunda yatatu nane sinikubwezele, 6 pakuti bwenji wanga wafika kuchokela kuulendo, ni ine nilibe chakudya chakumlandilila!’ 7 Ndiipo yujha wa mkati wamuyangha, ‘Usadanisaucha. Ndande nathomanga chicheko. Ine ni wanawanga tathogona, ni sinikhoza kuuka kuti nikupache chindhu chilichonjhe!’ 8 Zenedi nikukambilani, ingakhale siwauka ni kumpacha bumunda bwenji wake, nambho, chifuko mundhuyo wayendekela kumpembha, siwauke nikumpacha chilichonjhe icho wachifuna. 9 Chimwecho, ine nikukambilani, pembhani namwe simpachidwe, funafunani namwe simupate, gogodani, namwe simuchekulidwe chicheko. 10 Pakuti waliyonjhe uyo wapembha wapachidwa, uyo wafunafuna wapata, ni uyo wagogoda wachekulidwa chicheko. 11 Bwanji, ni tate yuti pakati panu uyo mwana wake wakampembha njhomba, wampacha njoka mmalo mwa njhomba? 12 Kapina mwana wakapembha zila wampache chipilili? 13 Chipano ngati anyiimwe, yawo muli wolakwa, mujhiwa kwapacha wana wanu vindhu vabwino, zenedi Atate wanu wakumwamba sayendekele kupunda kwapacha Mzimu Woyela yawo ampembha."

Yesu ni Belizabuli

14 Siku limojhi Yesu wamatochocha chiwanda chidamchita mundhu mmojhi kukala bubu. Basi, chiwanda yapo chidamchoka yujha mundhu wadali bubu wadayamba, ni gulu la wandhu lidazizwa. 15 Nambho, wina adakamba, "Wavichocha viwanda kwa nghongono za Belizabuli, wamkulu wa viwanda." 16 Wina adamuyesa kumpembha wachite vizindikilo kuchoka kumwamba. 17 Nambho, pakuti Yesu wadayajhiwa maganizo yawo, wadakambila, "Wandhu wa Ufumu walionjhe uwo uchuchana wene kwa wene, ufumu umeneo sugawanyike, ni wandhu a mnyumba imojhi akachuchana achinawene kwa achinawene nyumba sapatukane. 18 Ngati ufumu wa satana wagawanyika wene kwa wene, ulamulilo wake siulimbe bwanji? Nikukambilani chimwechi pakuti anyiimwe munena kuti ine nichocha viwanda kwa mbhavu za Belizebuli. 19 Chipano ngati ine inchocha viwanda kwa nghongono za Belizebuli, ngha wochatila wanu achocha viwanda kwa mbhavu za yani? Achameneo nde sakulamuleni anyiimwe. 20 Nambho, ngati nichocha viwanda kwa mbhavu za Mnungu, Ndiipo jhiwani Ufumu wa Mnungu wawandikila."

21 "Mundhu wali ni nghongono uyo wali ni vida vojhe yapo walonda nyumba yake, chuma chake chonjhe chikhala ni nimtendele. 22 Nambho wakajha mundhu wambhavu kupitilila iye wakamuhundukila ni kumbula, watenga vida vake vonjhe ivo wamavikulupilila ni kuvigawa vyuma vake vonjhe. 23 Mundhu waliyonjhe uyo siwali pamojhi ni ine, ndekuti wachuchana niine, ni mundhu waliyonjhe uyo siwakusa pamojhi ni ine watomwaza."

Kubwela kwa chiwanda

24 "Chiwanda chikamchoka mundhu, chizungulilazungulila malo ya nghalambo yopande majhi ni kufunafuna malo yopumulila. Nambho yapo chilepela kupeza malo yo pumulila, chikamba chene, ‘Sinibwelele kukh omo kwanga uko nachoka.’ 25 Yapo chifika, chiipheza nyumba yalambulidwa ni kukonjedwa bwino. 26 Basi, chipita kwatenga na achanjake viwanda vina saba ivo vili voipa kupunda kupitilila icho, vonjhe vimlowa mundhu mmeneyo, mmathelo mundhu mmeneyo wakhala woipa kupitilila umo wadali poyamba."

Mwawi wa bwino

27 Yesu yapo wamakamba chimwecho, wamkazi mmojhi pakati pa gulu la wandhu lijha wadakweza mvekelo, nikukamba, "Wali ni mwawi wamkazi uyo wakubala iwe ni kukuyamwicha!" 28 Nambho Yesu wadayangha, "Ali ni mwawi kupunda yawo avela mawu ya Mnungu ni kuyachata."

Mbadwa uwo ukonda vizindikilo

29 Ndiipo, yapo gulu la wandhu lidayendekela kuchuluka, Yesu wadayamba kukamba, "Mbadwa Uwu ni woipa. Ufuna kuona vizindikilo, nambho sapachidwa chizindikilo chilichonjhe ingakhale chizindikilo icho cha Yona. 30 Ngati umo Yona wadali chizindikilo cha kwalangiza wandhu a ku Ninawi, chimwecho ndeumo Mwana wa Mundhu siwakalile chizindikilo kwa mbadwa uwu. 31 Siku la lamulo, fumukazi wa kusheba siwachokele kwalamula wandhu wa mbadwa uwu. Niiye siwakambe kuti mbadwa huu wolakwa. Pakuti iye wadachoka kutali wajha kuvechela mau ya kuzindikila ya mfumu solomoni, nambho, pano walipo wamkulu kupitilila Solomoni. 32 Siku la ukumu, wandhu aku Ninawi siaime kuulamula mbadwa huu. Ndande anyiiwo adalapa ndande yona wadaauzila, nambho pano walipo wamkulu kupitilila Yona."

Nyali ya thupi

33 "Palibe mundhu uyo wawasha nyali ni kuivinikila mphika, nambho waika pamwamba pamalo poikila nyali kuti uyo walowa mmenemo wakhoze kuona. 34 Diso lako ni nyali ya thupi lako. Ngati diso lako lili labwino, thupi lako lonjhe siliwalilidwe. Nambho ngati maso yako silipenya, thupi lako nalo likhala mumdima. 35 Chimwecho, ukhale maso kuti dangalila ilo lili mkati mwako lisadakhala mdima. 36 Basi, ngati thupi lako lonjhe lajhala dangalila, popande chiwalo chalichonje icho chili ni mdima, basi thupi limenelo siliwale bwino ngati umo nyali iwalila."

Yesu wanyindila Afalisayo ni oyaluza a thauko

37 Yesu yapo wadamaliza kukamba yameneyo, Mfalisayo mmojhi wadamlalika kunyumba kwake kuti wakadye chakudya. Yesu wadapita kudya chakudya. 38 Nambho Mfalisayo mmeneyo wadazizwa yapo wadaona Yesu wakudya popande kusamba mmanja. 39 Ambuye adamkambila, "Anyiimwe Afalisayo mchuka vikho ni mbale kubwalo, nambho mkati mwanu mwajhala ludyo ni kuipa. 40 Achi sabobwa anyiimwe! Bwanji, uyo wadakonjani kubwalo osati nde uyo wadakukonjani mkati? 41 Chimwecho, vonjhe ivo mulinavo apacheni osauka, nianyiimwe simvomelezedwe pa chikhalidwe chomlambila Mnungu."

42 "Nambho, mavuto yakhale kwa anyiimwe Afalisayo, pakuti chifuko simufuna kwachitila wina ubwino ni kumkonda Mnungu. Nambho, mumchochela Mnungu fungo limojhi pakati pamafungo khumi ya thelele, ni vindhu vokomecha thelele. Mufunika kwachitila wina bwino ni kumkonda Mnungu, pamojhi ni kuchocha fungo limojhi pakati pa mafungo khumi. 43 Mavuto yakhale kwa anyiimwe Afalisayo, chifuko mukonda kukhala mmipando ya pachogolo, mnyumba yophezelana Ayahudi, ni kulonjeledwa kwa ulemu ni wandhu patandhandala. 44 Mavuto yali kwa anyiimwe chifuko muli ngati manda yayo siyadaikidwe chizindikilo, yayo wandhu ayaponda pamwamba pake popande kuyajhiwa."

45 Mundhu mmojhi pakati pa oyaluza thauko, wadayangha, "Oyaluza, yapo mkamba chimwecho simtitukwana ni ife?" 46 Yesu wadayangha, "Mavuto yakhale kwa anyimwe oyaluza thauko, chifuko mwaasenjha wandhu makatundu yolemela yayo sangakhoze kuyatenga, nimwachinawene wake simwathangatila kusenjhela kapina kugafya. 47 Mavuto yakhale kwa anyiimwe, chifukwa anyiimwe mwawakila viliza alosi yawo adapedwa ni achatate wanu. 48 Chimwecho, anyiimwe ni mboni ni mchimikiza chijha adachita achatate wanu, pakuti anyiiwo adapha alosi, ni anyiimwe mwawakila viliza vao, nambho simuchata yayo ayalalikila. 49 Chifuko cha ili, Mnungu pa kuzindikila kwake wadakamba, ‘Sinatumile alosi ni atumwi, nambho anjake saphedwe ni wina savutichidwe.’ 50 Chipano, anyiimwe mwaleledwa chimwechi ni anyiyao achogolela, simlangidwe chifuko cha nyifa ya alosi wonjhe yawo adaphedwa kuyambila kuumbidwa kwa jhiko, 51 kuyambila yapo wadaphedwa Abeli mbaka yapo wadaphendwa Zakaliya, uyo wadaphedwa pakati paguwa la njhembe yophyeleza Mnyumba ya Mnungu. Nikukambilani anyiimwe mwaleledwa chimwechi, simlangidwe chifuko cha ivi vonjhe."

52 "Mavuto yakhale kwa anyiimwe oyaluza athauko, chifuko anyiimwe mwachelekeza wandhu kuti sadamjhiwa Mnungu, ni mwachinawene simdamjhiwe, ni anyiwajha afuna kumjhiwa Mnungu mwachelekeza kuti sadamjhiwa."

53 Yapo Yesu wadachoka pamenemo, oyaluza thauko ni Afalisayo adayamba kumchucha kwa mbhavu ni kumfunjha mafunjho yambili, 54 ndande yakuti amgwile kwa mau yake kuti amlovye mmilandu.

Veja também

Publicidade
Bíblia Online Bíblia Online

Bíblia Online • Versão: 2026-06-18_14-04-22-