1 Yesu yapo wadamaliza kwakambila wandhu mawu yameneyo, wadachoka kupita ku Kapenaumu. 2 Kumeneko kudali wamkulu wa gulu la asilikali mwina uyo wadali ni mbowa wake uyo wamamkonda kupunda. Mbowa mmeneyu wadali wodwala pafupi kumwalila. 3 Wamkulu wa asilikali yujha yapo wadavela nghani za Yesu, wadaatuma azee wina wa Ayahudi, apite akampemphe kuti wamlamiche mbowa wake. 4 Yapo adafika kwa Yesu, adampempha kupunda, pokamba, "Mundhu uyu wafunikadi wathangatilidwe, 5 pakuti walikonda jhiko latu, ni iye watimangila, nyumba yopezanilana." 6 Ndiipo, Yesu wadapita pamojhi naanyaiwo. Yapo adawandikila kufika pakhomo pa yujha wamkulu wa asilikali, wamkulu wa gulu la asilikali wadaatuma achabwenji wake kwaiye amkambile, "Ambuye, msadajhichaucha kupunda, ndande ine siniloledwa kukulovyani imwe mnyumba mwanga. 7 Ndendande sinidajhione kuti ine nikhoza kujha kwanu imwe. Nambho kambani mawupe, ni mbowa wanga siwalame. 8 Pakuti inenjho ni mundhu uyo nili panjhi pa lamulo, ni nili ni asilikali panjhi panga, yao avela icho naakambila. Nikamkambila mmojhi, ‘Pita,’ iye wapita. Ni wina nimutana, ‘Majha,’ Nayonjho wakujha. Ni mbowa wanga nikamkambila, ‘Chita chimwechi,’ nayonjho wachita."
9 Yesu yapo wadavela chimwechi wadazizwa, naye wadang'anamukila wandhu ambili yawo amamchata ni kwakambila, "Sinidaonepo chikhulupililo chachikulu ngati ichi ata pakati pa wandhu a Yelusalemu."
10 Wandhu wajha adatumidwa kwa Yesu, yapo adafika kukhomo kwa wamkulu wa asilikali adampheza mbowa wake watholama.
11 Yapo wadamaliza yameneyo, Yesu wadapita ku mujhi umojhi uwo utanidwa Nayini, pamojhi ni oyaluzidwa wake ni gulu lalikulu la wandhu yawo wadachogozana nawo. 12 Ndiipo, Yesu yapo wadali pafupi kufika pa chicheko chachikulu cha mujhi, adatulukila wandhu yawo adatenga chitanda cha wammuna mmojhi. Mwana mmweyo wadali wa maye uyo wadafedwa ni wammuna. Ni wandhu ambili a mujhi ujha adali pamojhi ni wamkaziyo. 13 Ambuye Yesu yapo adamuona maye wa mwana yujha, adamlengela lisungu, adakamba, "Osalile." 14 Ndiipo, wadapita ni kuligafya bokosi la chitanda chijha, wandhu yawo adalitenga, adayima. Ndiipo wadanena, "Mnyamata iwe, nikukambila, nyakuka!" 15 Mnyamata wakufa yujha wadanyakuka, ni kukhala, ndiipo wadayamba kunena. Ndiipo Yesu wadampeleka kwa amaye wake. 16 Wandhu wonjhe adali pamenepo adadabwa, nikuyamba kumtamanda Mnungu, naakamba kuti, "Mneneli wamkulu wationekela pakati pathu. Mnungu wafika kwaombola wandhu wake." 17 Nghani zimezi zidaenela ku Yudea pamojhi ni malo yayo yadali pafupi, ni mayiko ina.
18 Oyaluzidwa a Yohana adamkambila Yohana yonjhe yayo wamachita Yesu. Nayo, wadaatana awili pakati pa oyaluzidwa wake, 19 wadaatuma apite kwa Ambuye Yesu akamfunjhe, "Bwanji, iwe nde Ambuye wajha akujha, kapina timlindilile mwina?" 20 Oyaluzidwa wajha yapo adafika kwa Yesu adanena, "Yohana mbatizi watituma kwanu tikufunjheni kuti imwe nde Ambuye wajha akujha, kapina timlindile mwina?" 21 Ndhawi imeneyo, Yesu wamalamicha wandhu yawo adali ni matenda yambili ni yawo azamwa ni viwanda, ni kuchita osapenya kuti apenye. 22 Basi, Yesu wadayangha, "Pitani mkamkambile Yohana yaya yonjhe muyaona ni kuyavela. Osapenya apenya, andendele ayenda, amakate ayelesedwa, osavela avela, akufa auka, ni osauka alalikidwa Uthenga Wabwino. 23 Wali ni mwawi mundhu yujha siwanikhaikila!"
24 Anyiwajha wandhu adatumidwa ni Yohana yapo adachoka, Yesu wadayamba kulikambila gulu la wandhu nghani za Yohana, niwakamba, "Bwanji, yapo mudapita kumuona Yohana kuphululu kujha, mudakhulupilila kuona chiyani? Bwanji, mdapita kuona bango nilitingizidwa ni mbhepo? 25 Bwanji, mudapita kuona chiyani? Bwanji, dapita kumuona mundhu uyo wavala njhalu za mtengo waukulu? Notho! Anyiyawo avala njhalu ngati zimenezo, nikudyelela umoyo waufulu, akhala mnyumba ya mafumu, sakhala mthengo! 26 Nambho, mudapita kuona chiyani? Bwanji, mudapita kumuona mlosi? Yetu, mdapita kumuona mundhu wamkulu kupitilila mlosi. 27 Yohana mmeneyu ndeuyo nghani zake zalembedwa Mmalembo Yoyela,
‘Penya, sinimtume mthenga wanga wakuchogolele,
uyo wakukonjela njila yopita iwe.’ 28 Nikukambilani, pakati pa wandhu wonjhe abalidwa ni wachikazi, palibe uyo wali wamkulu kupitilila Yohana mbatizi. Nambho, uyo wali wamng'ono kwambili pa ufumu wa Mnungu wali wamkulu kupitilila Yohana."
29 Wandhu wonjhe pamojhi ni wolandila malipilo, anyiyawa adabatizidwa ni Yohana, yapo adavela nghani zimenezo adavomela kuti Mnungu ni wabwino. 30 Nambho a Falisayo ni oyaluza mathauko, adakana yayo adakambilidwa ni Mnungu kuti ayachite, yayo yadakonjedwa ndande yawo, adakana kubatizidwa ni Yohana. 31 Yesu wadayendekela kukamba, "Bwanji, sinalinganiche ni chiani, wandhu a mbadwa uno? Bwanji, wandhu anyiyawa ni amtundu wanji? 32 Ali ngati wana wokhala pamalo yayo amakomanilana wandhu, naatanana achinawene kwa achinawene wake,
‘Takutimbilani vitolilo, nambho simudavine!
Takuyimbilani nyimbo za zaya nambho simudalile!’
33 Pakuti Yohana mbatizi yapo wadafika, niwamanga kudya ni wosamwe divayi kila ndhawi, ni anyiimwe mudamnena kuti, ‘Wali ni viwanda!’ 34 Nayenjho mwana wa Mundhu wafika, wakudya ni wakumwa, namwe mkambanjho, ‘Muoneni uyu! Waludyo ni wolojhela, bwenji wa wolandila malipilo ni wochimwa!’ 35 Nambho, ekima ya Mnungu yavomelezewa kuti ni yabwino kwa wonjhe yawo ayivomela."
36 Siku limojhi, mfalisayo mmojhi wadamlalika Yesu kujha kudya chakudya cha ujhulo cha mnyumba mwake. Yesu nayonjho wadalowa mnyumba mwa mfalisayo yujha, wadakhala pa chitembwe ni kudya chakudya. 37 Ndiipo, mmujhi ujha mudali wamkazi mmojhi uyo wadali wochimwa. Yapo wadavela kuti Yesu watokudya mnyumba ya mfalisayo, wadatenga njhupa iyo lidajhala mafuta yonunghila. 38 Wadakwatama kumbuyo kwa miyendo ya Yesu, uku niwalila, ni kukhatapicha miyendo ya Yesu kwa misozi yake. Wamkazi yujha wadamchangula miyendo ya Yesu ni machichi yake. Wadaibusu miyendo ya Yesu ni kuyinyeka mafuta. 39 Mfalisayo yujha wadamlalika Yesu yapo wadaona chimwechio, wadaganizila mumtima mwake, niwakamba, "Ngati mundhu uyu wadakakhaladi mlosi wadakamjhiwa kuti uyu wamkaziyu wagafya ni wamtundu wanji, yakuti ni wochimwa." 40 Yesu wadamkambila Mfalisayo mmeneyo, "Simoni, nili ni kandhu kakukambila." Simoni nayenjho wadayangha, "Yetu oyaluza, kambani." Yesu wadakamba, 41 "Kudali ni wandhu awili adakongola ndalama kwa mundhu uyo wamakongolecha, 500 ulingana ni mkokolo wa pachidwa mundhu wakachita njito kwa siku 500, mwinayu wadatenga makobili 50, ulingana ni mkokolo wapachidwa mundhu wakachita njito kwa siku 50. 42 Yapo adalepela kubweza ndalama zake, wadaalekelela wonjhe awili. Chipano, pakati pa awiliwa yuti siwamkonde kupunda mundhu yujha wadakongoza ndalama?" 43 Simoni wadayangha, "Niganiza, mundhu yujha walekeleledwa ngongole yayikulu kupunda, nde uyo siwamkonde kupunda mundhu yujha wokongoza."
Yesu wadakamba, "Wayangha bwino." 44 Ndiipo Yesu wadamng'anamukila wamkazi yujha ni kumkambila Simoni, "Bwanji, umuona wamkazi uyu? Yapo nidalowa pakhomo pako pano sudanipache maji yosamba mmyendo yanga, nambho yamkazi uyu wanichuka myendo yanga kwa misozi yake ni kunichangula kwa machichi yake. 45 Nambho iwe sudanilonjele kwa kunikumbatila, nambho chiyambile nalowa muno, wamkazi uyu siwadaleke kunibusu myendo yanga. 46 Iwe sudanipake mafuta mmutu mwanga, nambho wamkazi uyu wanipaka mafuta mmyendo yanga. 47 Chimwecho, nikukambila machimo yake yayo yadali yambili yalekeleledwa pakuti walangiza chikondi chachikulu. Nambho uyo walekeleldwa pang'ono, wakonda pang'ono." 48 Ndiipo, Yesu wadamkambila wamkazi yujha, "Walekeleledwa machimo yako." 49 Wandhu wina adalipo pajha, adakambilana, "Mundhu uyu ni yani, uyo wakhoza kwalekelela wandhu machimo yawo?" 50 Yesu wadamkambila wamkazi yujha, "Chikhulupililo chako chakulamicha, upite kwa mtendele."