1 Yesu yapo wamachoka kubwalo kwa kunyumba ya Mnungu, oyaluzidwa wake mmohji wadamkambila, "Oyaluza, penyani myala iyi ni nyumba izi umo zakadwila!" 2 Yesu wadamuyangha, "Bwanji, uzizizwa nyumba izi umo zakulila? Palibe ata mwala umojhi uwo siukhalile pamwamba pa wina, kila mwala siugomoledwe."
3 Yesu yapo wadakhala pamwamba pa phili la Mizeituni, kuchijya la Nyumba ya Mnungu, pamenepo Petulo ni Yakobo ni Yohana ni Andulea adamfunjha yapo adali pawokha, 4 "Mtikambile vindhu vimenevo sivichokele siku lanji? Ni chizindikilo chanji icho sichilangize kuti vindhu vimenevo vili pafupi kujha?"
5 Yesu wadayamba kwakambila, "Mkhalemaso mundhu waliyonjhe siwadakunyengani. 6 Wandhu ambili siajhe niatumila jhina langa, nikukamba mthila, ‘Ine nde Kilisito.’ Ni siwaanyenge wandhu ambili. 7 Yapo simvele nghani za nghondo, ni mbili za nghondo, simudaopa. Vindhu vimenevo lazima vichokele, nambho mathelo yakali siyadafike. 8 Wandhu ajhiko limojhi siabulane ni wandhu ajhiko lina, ufumu umojhi siubulane ni ufumu wina, kumalo kwambili sikukhale ni chimtingiza cha ndhaka ni njala yaikulu. Yaya yonjhe siyakhale ngati chiyambo cha uchungu wa kujhimasula mwana."
9 "Nambho anyiimwe mkhale maso. Pakuti wandhu saakugwileni ni kukupelekani ku bwalo la milandu. Saakubuleni ku nyumba zokomanilana Ayahudi. Simpelekedwe kwa alamuli ni mafumu ndande ya ine, kuti mwalalikile Uthenga Wabwino. 10 Mathelo yakali osafike, Uthenga Wabwino ufunika ulalikidwe mmayiko yonjhe. 11 Yapo siakugwileni ni kukupelekani ku bwalo la milandu, msadaganizila chokamba. Ndhawi ikajha kambani chalinjhonjhe icho simpachidwe, pakuti osati anyiimwe simkambe nambho Mzimu Woyela. 12 Ndhawi imeneyo mbale siwamchoche mbale wake wapedwe, ni tate siwamchoche mwana wake wapedwe, wana nao ni siabula obala wao ni kuwapha. 13 Wandhu wonjhe siakuipileni anyiimwe ndande munichata ine. Nambho uyo siwalimbe mtima mpaka potela nde uyo siwaomboledwe."
14 "Yapo simuone, Chindhu cha kumdingha Mnungu, chili munyumba ya Mnungu, pamenepo, anyiawo ali ku jhiko la Yudea athawile kuphili, mundhu uyo wasoma wajhiwe mate yake. 15 Mundhu waliyonjhe uyo wali kubwalo kwa nyumba yake siwadalowa mkati kutenga chindhu chilichonjhe. 16 Mundhu uyo wali kumunda siwadabwela kukhomo kutenga njhalu yake. 17 Savutike kupunda anyamaye yawo ali ni pathupi ni oyamwicha siku zimenezo! 18 Apembheni a Mnungu kuti vindhu vimenevo sividachokela nyengo yozizila. 19 Siku zimenezo sikukhale ni mavuto yayo siyadachokelepo kuyambila yapo Mnungu wadaumba jhiko mbaka chipano, ni siyachokelanjho. 20 Ngati Ambuye siadakazichepecha siku zimenezo palibe mundhu uyo wadakalama. Nambho ndande ya wandhu wake wasangha, Ambuye siazichepeche siku zimenezo."
21 "Pa masiku yameneyo mundhu waliyonjhe wakakumbilani, ‘Kilisito Muomboli wali pano,’ kapina, ‘Wali yapo,’ simdakhulupilila. 22 Pakuti siachokele Alosi amthila ni wandhu ajhitana, ‘Ine ni Kilisito!’ Siachite vizindikilo ni vodabwicha, kuti ngati ikakhozekana anyenge wandhu asanghidwa ni Mnungu. 23 Khalani maso! Ine nakukambilani kila chindhu icho sichichokele."
24 "Ndiipo, siku zimenezo, yapo siyathe mavuto yameneyo, jhuwa silikhale mdima ni mwezi siuchocha dangalila. 25 Ndhondwa sizigwe kuchokela kumlengalenga, ni vindhu ivo vili kumlengalenga sivitingizidwe. 26 Pamenepo wandhu sianione ine Mwana wa Mundhu, ninijha nili mmitambo kwa mbhavu zambili ni ulemelelo. 27 Ndiipo sinaatume atumiki akumwamba wakuse wandhu wanga nidaasangha kuchokela kumadela yonjhe yanayi ya jhiko, kuchokela mmathelo ya jhiko, mbaka mmathelo ya kumwamba."
28 "Jhiyaluzeni chifani ichi kuchokela kwa mtengo wa mtini, ndhawi zake yapo ziyamba kuphukila ni kuchocha machamba, mjhiwa kuti nyengo ya mwavu yawandikila. 29 Chinchijha yapo simuone vindhu ivo nidakukambilani ni vichokela, jhiwani kuti ine mwana wa Mundhu niwandikila kujha. 30 Nikukambilani uzene, wandhu a mbadwa uwu siumwalila mbaka yaya yonjhe yachokele. 31 Kumwamba ni jhiko sivimwalile, nambho mawuyanga siyakhale muyaya."
32 "Palibe mundhu waliyonjhe wajhiwa, siku kapina ndhawi imeneyo ata atumiki akumwamba kapina ine mwana wa Mnungu, nambho Mnungu yokha, nde uyo wajhiwa. 33 Mkhale maso ni mchezelele, ndande simjhiwa wabwela ndhawi yanji. 34 Ilingana ni mundhu uyo wadachoka ni kupita kuulendo, kwasiila akapolo wake alonde kila chindhu, kila mundhu wadampacha njhito yake yopota. Ni wadamlamula mlonda wa pakhomo wakhale maso. 35 Chimwecho mchezelele, pakuti simjhiwa liti mwene nyumba siwabwele, siwabwele ujhulo, kapina usiku pakati kapina tambala yapo siwalile, kapina umawa. 36 Wakabwela kwa chizulumukila siwadakupezani mwagona. 37 Ichi nikukambilani anyiimwe, chimchijha naakambila wandhu wonjhe. Mkhale maso!"