Publicidade

Marcos 14

Njila yakumpha Yesu

1 Zidakhalila siku ziwili kulowa siku la pwando la Pasaka ni ya mabumunda yayo siidathilidwe amila. Wakuluakulu a ajhukulu, ni oyaluza athauko amamafuna funa njila ya kumgwila Yesu kwa chisisi ni kumpha. 2 Adakamba, "Sitidamgwila ndhawi ya pwando la Pasaka, pakuti wandhu akhoza kuchita fujho."

Wamkazi wamnyeka Yesu mafuta ku Besania

3 Yesu wadali ku Besania kukhomo kwa Simoni, uyo wadali ni makate. Yapo amadya chakudya cha ujhulo, wamkazi mmohji, uyo wadali ni njhupa iyo idali ni mafuta yonunghila ya mtengo wa ukulu, wadajha, wadamasula ijha njhupa ni kumpungulila Yesu kumutu. 4 Wandhu akumohji adali pamenepo adakwiya, adakambilana, "Ndande yanji wawananga mafuta ya mtengo waukulu kupunda? 5 Mbasa yadakagulichidwa kwa mtengo waukulu kupunda, ni ndalama zimenezo kwapacha osauka." Ndiipo adamnyindila yujha wamkazi.

6 Nambho Yesu wadaakambila, "Msiyeni! Ndande yanji mumchaucha? Iye wanichitila chindhu cha bwino. 7 Wandhu osauka mulinao siku zonjhe, mkhoza kwathangatila ndhawi yaliyonjhe yapo mfuna. Nambho ine sinikhala ni anyiimwe siku zonjhe. 8 Wamkazi uyu wachita umo wakhozela, ni wachogolela kulinyeka thupi langa mafuta ndande yo kulikonjekela likali losazikidwe 9 Nikukambilani uzene, paliponjhe pajhiko Uthenga Wabwino yapo siilalikidwe, chindhu ichi wachichita uyu maye sichichuludwe kwa kumkumbukila Iye."

Yuda wavomela kumng'anamuka Yesu

10 Ndiipo, Yuda isikaliyote, mmojhi wawajha oyaluzidwa khumi ni awili, wadapita kwa wakulu wa jhukulu kuti wamng'anamuke Yesu kwa anyiiwo. 11 Wakuluakulu wa ajhukulu yapo adavela nghani zimenezo, adakondwa, adamwahidi kumpacha ndalama. Ndiipo, yuda wadayamba kufunafuna malo ya kumng'anamuka Yesu.

Yesu wakudya chakudya cha Pasaka ni oyaluzidwa wake

12 Pa siku loyamba la pwando la mabumunda yayo yalibe amila, ni siku la kumpha mwana wambelele wa Pasaka, oyaluzidwa wake adamfunjha, "Bwanji, ufuna tipite kuti tikukonjele pwando la Pasaka?"

13 Yesu wadaatuma oyaluzidwa wake awili, wadaakambila, "Pitani kumujhi, kumeneko simummpheze wammuna mmojhi watenga mchuko. Mchateni mundhu mmeneyo, 14 mbaka mnyumba iyo siwalowe, ndiipo mkamkambile mwene nyumba, ‘Oyaluza afunjha, bwanji, chili kuti chumba cha alendo kuti nidye chakudya cha Pasaka pamojhi ni oyaluzidwa wanga?’ 15 Iye siwakulangizeni chumba chachikulu kugholofa icho chakonjekeledwa bwino ni kupambidwa. Tikonjekeleni mmenemo."

16 Oyaluzidwa adachoka, adapita kumujhi, adampeza kila chindhu chili ngati umo adakambilidwa ni Yesu. Adakonjekela chakudya cha Pasaka. 17 Ujhulo yapo udajha, Yesu wadafika pa nyumba ijha pamojhi ni oyaluzidwa wake khumi ni awili. 18 Yapo amadya, Yesu wadakambila, "Zenedi nikukambilani mmojhi pakati panu uyo wakudya niine, siwaning'anamuke." 19 Anyiwajha oyaluzidwa wake adayamba kudandaula, kila mmojhi wadamfunjha, "Bwanji, unikamba ine nde sinikung'anamuke?" 20 Yesu wadaayangha, "Mmojhi wa anyiimwe khumi ni awili, uyo wasunjhila bumunda bakuli imohji ni ine. 21 Ine mwana wa Mundhu sinimwalile ngati umo yalembedwela Malembo Yoyela. Nambho siwavutike mundhu yujha siwaning'anamuke ine mwana wa Mundhu, idakakhala mbasa mundhu mmeneyo siwadakabadwa!"

Chakudya cha Ambuye

22 Yapo amadya, Yesu wadatenga bumunda, wadamuyamika Munungu, wadaubandhula ni kwapacha oyaluzidwa wake uku ni wakamba, "Tengani, mudye ili ni thupi langa." 23 Ndiipo wadatenga chikho cha divai, wadamuyamika Mnungu, wadaapacha, wonjhe adachimwela. 24 Wadaakambila, "Uwu ni mwazi wanga uwo uchimikiza chipangano cha Mnungu, mwazi uwo umwazika ndande ya wandhu ambili. 25 Zenedi ni kukambilani, sinimwa divai mbaka siku lijha yapo siniimwenjho divai yachipano ku Ufumu wa Mnungu." 26 Ndiipo adaimba nyimbo ya kumtamanda Mnungu yapo adamaliza kuimba, adachoka ni kupita ku phili la Mizeituni.

Yesu walosa kuti Petulo siwamkane

27 Yapo adali mnjila Yesu wadaakambila oyaluzidwa wake, "Anyiimwe mwaonjhe simunithawe ni kunisiya ngati umo yalembedwela mmalembo Yoyela,

‘Mnungu siwambule owesa,

ni mbelele zonjhe sizimwazikane.’

28 Nambho nikatho hyuka sinikuchogoleleni kupita ku Galilaya." 29 Chimwecho Petulo wadamkambila, "Ata ngati wonjhewa akakusiyani, nambho ine sinikusiyani." 30 Yesu wadamkambila Petulo, "Zene nikukambila, usiku wa lelo tambala wakali osalile mala kawili, siunikane mala katatu." 31 Nambho Petulo wadachimikiza kokamba, "Ata ngati ikafunika nife pamojhi ni imwe, sinikusiyani." Niwajha oyaluzidwa wina nao adakamba chimwecho.

Yesu wapembhela mbusitani ya Getisemane

32 Adafika pamalo yapo pamatanidwa Getisemane. Yesu wadaakambila oyaluzidwa wake, "Khalani yapa ine yapo nipita kupembhela." 33 Ndiipo wadaatenga Petulo ni Yohana ni Yakobo, wadapita nao patali pang'ono, wadavela kupweteka mumtima ni kulaga. 34 Wadaakambila, "Nili ni chisoni kupunda mumtima mwanga, chikhoza kunipha. Khalani yapa ni mchezelele." 35 Yesu wadapita pachogolo pang'ono, wadajhitaya panjhi chifufumimba, uku ni wapembha, "Ngati ikakhozekana sinidapitila saa iyi ya mavuto." 36 Wadapembha, "Atate wanga, kwanu vindhu vonjhe vikhozekana. Mnichochele chikho ichi cha mavuto, nambho isidakhala ngati umo nifunila ine, nambho ngati umo mfunila imwe."

37 Ndiipo yapo wadabwela wadaapheza oyaluzidwa wake atatu agona. Basi wadamfunjha Simoni uyo watanidwa Petulo, "Simoni wagona litulo? Siudakhoze kuchezelela ata saa imojhipe?" 38 Ndiipo, wadaakambila, "Mchezelele ni mpembhele kuti simdayesedwa kuchita voipa. Anyiimwe mfuna kulimbila mtima mayeso nambho matupi yanu yalibe mbhavu."

39 Yesu wadapitanjho kupembhela uku niwakamba mawu yamweyajha. 40 Ndiipo, wadaajhelanjho, ni wadaapheza agona, maso yao yadali ni litulo. Siadajhiwe cha kumuyangha.

41 Yapo wadaajhela mala ya katatu wadaakambila, "Mkali kugona ni kupumulila? Ukani! Saa yathofika! Ine mwana wa Mundhu siniikidwe mmanja mwa wandhu amachimo. 42 Nyakukani! Tijhipita! Mundhu uyo siwaning'anamuke wali pampano."

Yesu wagwilidwa

43 Yesu yapo wadali wakali kukamba, Yuda mmojhi wa anyiwajha oyaluzidwa khumi ni awili, wadafika. Wadajha pamojhi ni gulu la wandhu anyiawo adali ni maupanga ni vibonga. Adatumidwa ni wakulu wa ajhukulu ni oyaluza athauko ni achogoleli. 44 Ndiipo Yuda yujha wadang'anamuka wadaapacha chizindikilo, wadaakambila, "Mundhu uyo sinimbusu nde mumfuna. Mgwileni ni kumuika pa ulonda, wasadathawa."

45 Pampajha Yuda yapo wadafika, wadamchata Yesu, ni wadamlonjela, "Oyaluza!" Ndiipo wadambusu. 46 Ndiipo, wandhu wajha adamgwila Yesu ni kumuika panjhi pa ulonda. 47 Nambho mmojhi wa wandhu waanyiwajha adaima pamojhi ni Yesu, wadasolomola upanga wake, wadamdula khutu mbowa wa mjhukulu wamkulu. 48 Yesu wadaafunjha, "Bwanji, mwajha pano ni maupanga ni vibonga kunigwila ine ngati mnghungu? 49 Kila siku nidali pamojhi ni anyiimwe uku niyaluza panyumba ya Mnungu, simdanigwile. Nambho yaya yachitika kuti Malembo Yoyela yakwanile."

50 Pamenepo oyaluzidwa wonjhe adamsiya ni kuthawa.

51 Kudali ni mnyamata mmojhi wadavala shukape wamamchata Yesu. Yapo amafuna kumgwila, 52 wadasiya shuka lake ni kuthawa popande kuvala.

Yesu pachogolo pa bwalo la milandu

53 Ndiipo, adampeleka Yesu ku nyumba ya mjhukulu wa mkulu, pamenepo ajhukulu waakulu wonjhe, achogoleli ni oyaluza thauko adaphezana pamojhi. 54 Petulo wamamchata Yesu kwa patali, wadalowa mseli ya mjhukulu wamkulu, wadakhala pamojhi ni alonda uku ni wamatoothela moto. 55 Ajhukulu waakulu, ni wandhu wonjhe abwalo la milandu adafunafuna umboni wa kumpacha Yesu mlandu, kuti akhoze kumpha nambho siadaupate.

56 Wandhu ambili adachocha umboni wa mthila kwa Yesu, nambho umboni wao siudalingane. 57 Ndiipo wandhu wina adaima, ni kuchocha umboni wamthila niakamba, 58 "Tidamvela mundhu uyu ni wakamba, ‘Sinigomole nyumba iyi ya Mnungu yamagwidwa kwa manja ya wandhu. Ni kwa masiku yatatu siniimange yina iyo siimangidwa kwa manja ya wandhu.’ " 59 Nambho ata chimwecho umboni wao siudalingane.

60 Ndiipo, mjhukulu wamkulu wadaima pachogolo pa wandhu ni kumfujha Yesu, "Bwanji, siuyangha kandhu? Bwaji siuona kuti wandhu wonjhe yawa achocha umboni wa kukupacha mlandu iwe?" 61 Nambho Yesu wadakhala chete, siwadakambe kandhu. Mjhukulu wamkulu wadamfunjhanjho, "Bwanji iwe nde Kilisito, Mwana wa Mnungu uyo watamandidwa?" 62 Yesu wadamuyangha, "Nde ine. Ni anyiimwe simumuone ine mwana wa Mundhu nakhala janja la kwene la Mnungu wambhavu, ninijha mmitambo ya kumwamba." 63 Mjhukulu wamkulu wadang'amba njhalu zake kulangiza mbwayi ni kukamba, "Bwanji, tifunanjho amboni a chiyani? 64 Mwachinawene mwavela umo wamkafulila Mnungu" Anyiimwe muona bwanji? Bwalo lonjhe lidamlamula waphedwe. 65 Ndiipo wandhu wina adayamba kumlavulila Yesu malovu, adamcheka maso, adambula ni adamkambila, "Losa yani wakubula," Chinchijha alonda nawo adamtenga ni kumbula.

Petulo wamkana Yesu

66 Petulo yapo wadali wakali panjhi mseli, wamkazi mmojhi mbowa wa mjhukulu wamkulu wadajha. 67 Yapo wadamuona Petulo ni waotha moto, wadampenyechecha, ni kumkambila, "Chimchijha iwe nawe udali pamojhi ni Yesu wa ku Nazaleti." 68 Nambho Petulo wadakana, "Sinimjhiwa ni sinichijhiwa icho uchikamba." Ndiipo Petulo wadatuluka kubwalo mbaka kuseli. Pampajha tambala wadalila. 69 Yujha mbowa yapo wadamwonanjho Petulo pamalo pajha, wadayamba kwaakambila wandhu wajha adaima pamenepo kuti, "Mundhu uyu nayo ni mmojhi wao." 70 Nambho Petulo wadakananjho.

Pambuyo pang'ono, wandhu wajha adaima pamenepo adampitila ni adamkambila Petulo, "Zenedi iwe ni mmojhi wao, pakuti iwe ni mundhu wa ku Galilaya." 71 Chimwecho Petulo wadayamba kujhileswa ni kujhilumbilila, "Ine sinijhiwa mundhu mmeneyo mumkamba nghani zake." 72 Pampajha tambala wadalila mala ya kawili. Ndiipo Petulo wadakumbukila umo Yesu wadamkambila, "Tambala wakali siwadalile mala kawili, siunikane mala katatu." Chimwecho Petulo wadayamba kulila.

Veja também

Publicidade
Marcos
Ver todos os capítulos de Marcos
Bíblia Online Bíblia Online

Bíblia Online • Versão: 2026-06-18_14-04-22-