1 Mnungu watituma ife tikakambile wandhu wake uthenga uwo wandhu siwadakambilepo wandhu, taikidwa kukhala oyimilila nghani za chikhulupi cha Mnungu. 2 Chifunika kwa mtumiki ni kukhala wokhulupilila. 3 Nambho kwanga siyo kandhu kuti nilamulidwe ni anyimwe, kapina nyumba za milandu, ngati nachita njhito bwino kapina osati bwino, nambho sinijhilamula namwene. 4 Pakuti sinijhiwa ngati nachita chindhu choipa, nambho siilangiza kuti ine nilibe mlandu, nambho yao anilamula ine ni Ambuye. 5 Chimwecho, msadamlamula mundhu walionjhe ndhawi yake ikali osafike, lindani mbaka yapo Ambuye siwajhe. Iye siwayaike pa dangalila yayo yadabisidwa kumdima, ni kuika padangalila yayo yali mumtima mwa wandhu. Ndhawi imeneyo kila mmojhi siwalandile matamando kuchokela kwa Mnungu.
6 Achabale wanga, vindhu vimenevo navichita kukhala chifani cha ine ni Apolo dala yakuthangatileni, dala kwa chifani chathu, "Kuyavela nikuyachita yayo yalembedwa." Mmojhi wanu wasadajhi dama ni kumdelela njake. 7 Yani wakuchita ukhale wamkulu kupitilila m wina, bwanji Mnungu siwadakupache kilakandhu icho ulinacho? Chabwino, ngati udalandila ujhidama chiyani?
8 Bwanji, mwathokhala nikila kandhu yako mufuna? Mwathokhala opata? Mwathokhala mafumu, chabwino, idakakhala bwino ngati mudakhala mafumu ili nafe tikhale mafumu pamojhi namwe. 9 Niganiza kuti Mnungu watichocha ife atumwi mmathelo, ngati wandhu yawo alangidwa kuphedwa pa ndhandala, ndande takhala chosekechela kwa wandhu wonjhe, kwa atumiki a Mnungu akumwamba ni wandhu. 10 Ife tionekana ngati masabwabwa ndande ya kumtumikila Kilisito, nambho anyiimwe nianjelu mwa Kilisito, ife ofooka, nambho anyiimwe muli nimbhavu, ulemelelo, nambho ife sitipata ulemu. 11 Ata ndhawi ino, tili ni njala ni lujho, tilibe njhalu, tibulidwa, nitilibe pokhala, 12 ndiipo tijhivuticha kupota njhito kwa manja yathu. Akatitukana taachitila vabwino, akatikwiicha talekelela, 13 akatitukwana, ifetayangha kwa mau yabwino, nitichichidwa ngati wandhu wopande mate pano pajhiko.
14 Nilemba yaya osati ndande ya kukulengechani njhoni, nambho ndande ya kukuyaluzani ngati wana yawo nikukondani. 15 Ata ngati muli ni oyaluza khumi elfu mwa Kilisito, nambho muli ni atate amojhi. Pakuti ine nde navomela mwa Kilisito Yesu, kukupelekelani Uthenga Wabwino. 16 Chimwecho, nikupembhani mchate chifano changa. 17 Nde ndande namtuma Timoseo kwanu, mwana uyo nimkonda, okhulupilika pakulunjana ni Ambuye, uyo siwakumbuche njila niichata pa kulunjana ni Kilisito, ngati mujha niyaluzila kila pamalo pa kila gulu lawandhu lamkhulupila Yesu.
18 Wina ayamba kukhala ambuli aganiza ngati sinijha kukuyendelani. 19 Ngati Ambuye akaniloleza, sinijhe kwanu msanga, nane sinijhiwe, osati mau laope anyiyawo ambuli, ila mbhavu zao. 20 Pakuti Ufumu wa Mnungu siukhala mmau, nambho kukhala ni mbhavu za Mnungu. 21 Anyiimwe msangha chiyani? Nijhe kwanu ni mkhwapulo, kapina nijhe mu chikondi ni mtima ofacha?