Publicidade

1 Coríntios 15

Kuhyuka kwa Yesu

1 Chipano nifuna kukumbuchani anyiimwe abale wanga, ujha Uthenga Wabwino nidakulalikilani, namwenjho mudaikhulupilila, ni kuima nganganga. 2 Kupitila Uthenga Wabwino mulamichidwa, ikakhala ngati mupotela njhito Uthenga uwo nidakulalikilani, ila ngati simusiye, kukhulupilila kwanu kudali kwachajhe.

3 Ine nidakupachani vindhu ivo nidavilandila, kuti Kilisito wadamwalila kwa ndande ya machimo yathu, ngati umo yalembedwela malembo ya Mnungu, 4 kuti wadazikidwa ni siku la katatu wadahyuka, ngati umoyalembedwela malembo ya Mnungu, 5 kuti wadamtulukila Kefa, ndiipo pambuyo wadaatulukila wajha khumi ni awili. 6 Pambuyo wadatulukila yawo amkhulipila Kilisito miathano, kwapamojhi, ambili wao akali amoyo, nambho wina adathomwalila. 7 Pambuyo wadamtulukila Yakobo, ndiipo wadatulukila atumwi wonjhe.

8 Pothela wadanitulukila ine Poolo uyo nidali ngati uyo wabadwa kwa njila yozizwicha. 9 Mateyake ine sinijhika ngati umo ajhiwikila atumwi wina, ni sinifunika kutanidwa mtumwi, ndande nidalivuticha gulu la wandhu amkhulupilila Yesu. 10 Nambho kwa ubwino wa Mnungu nali ngati umu nali, ni ubwino wake siudali chajhe, ine nachita njhito kupitilila atumwi wonjhe, osati ine nambho ubwino wa a Mnungu uchita njhito pamojhi ni ine. 11 Chimwecho, ikhale ine nidalalikila kapina anyiiwo atumwi wina adalakila Uthenga Wabwino, ata chimwecho taonjhe tilalikila Uthenga uwu uwo tidaukhulupilila.

Kuhyuka kwathu

12 Chipano, pakuti talalikila kuti Kilisito wadahyuka, mbona akumojhi wanu akamba wandhu akufa sahyuka? 13 Ngati palibe kuhyuka, basi ata Kilisito nayo siwadahyuke, 14 Ni ikakhala Kilisito siwadahyuke, basi kulalikila kwathu kulibe mate ni kukhulupilila kwanu kulibe mate. 15 Kupitilila yameneyo, ife tidakakhala amboni amthila pachogolo pa Mnungu, ndande tidakamba kuti Mnungu wadamhyukicha Kilisito, kumbe iye siwadamhyukiche, nambho limenelo silikhoza kukhala lazene kuti akufa siahyukichidwa. 16 Ikakhala zene wandhu akufa siahyukichidwa, ndekuti Kilisito nayo siwadahyukichidwe. 17 Ni ngati Kilisito siwada hyukichidwe, chikhulupi chanu nichachajhe, ni mkali mumachimo yanu. 18 Chimwecho ni onjhe anyiyao amwalila uku amkhulupila Kilisito atayika. 19 Ngati yajha tifuna kupata kuchoka kwa Kilisito ndande ya umoyo wathu wasazinope, ife ni wandhu tifunika kulengeledwa lisungu kupitilila wandhu onjhe pajhiko.

20 Nambho uzene Kilisito nde oyamba kuhyukichidwa ni Mnungu, kwa awajha amwalila ngati vipacho voyamba va mlimi. 21 Pakuti ngati mujha nyifa yapelekedwa pajhiko kupitila kwa mundhu mmojhi nde Adamu, chimwecho kuhyuka nako kwajha kupitila mundhu mmojhi nde Kilisito. 22 Ngati mujha kwa kulunjana ni Adamu wandhu wonjhe amwalila, chinchijha wonjhe sahyukichidwe kwa kulunjana ni Kilisito. 23 Nambho kila mmojhi siwahyuke kwa ndhawi yake, Kilisito wadali oyamba, nde sachatile anyiwajha ali wake ndhawi iyo siwajhe. 24 Pambuyo pa yameneyo, mathelo nde siyafike Kilisito yapo siwapache Amnungu Atate ufumu, pambuyo pa kutayila kutali kila mafumu, ulalilo ni mbhavu 25 Kilisito, wafunika walamulile, mbaka yapo Mnungu siwaike adani wake wonjhe panjhi pa ulamulilo wake. 26 Nyifa nde mdani wothela uyo siwayomwechedwe. 27 Malembo ya Mnungu yakamba, "Mnungu waika vindhu vonjhe panjhi pa ulamulilo wake." Nambho malembo yapo yakamba, "Vindhu vonjhe vaikidwa panjhi pa ulamulilo wake dala wavilamule" Ili ni mate Mnungu siwalowa gulu limenelo la vindhu, mate iye nde waviika vindhu vimenevo panjhi pa Kilisito. 28 Nambho vindhu vonjhe vikatho ikidwa panjhi pa ulamulilo wa Kilisito, nde yapo iye nayo Mwana siwajhiike panjhi pa ulamulilo wa Mnungu, uyo waika vonjhe panjhi pa ulamulilo wake, dala Mnungu walamulile vonjhe.

29 Ngati palibe kuhyuka, bwanji wandhu anyiyao abatizidwa ndande ya anyiyao amwalila, apenyelela kupata chiyani? Ngati yao amwalila siahyukichidwa, kubatizidwa ndande yao kuli ni mate yanji? 30 Niife ndande yanji tali muhatali ndhawi zonjhe? 31 Achabale, ine niichata nyifa siku zonjhe! Kwa ufulu nilinawo kwaanyiimwe pakulunjana ni Kililsito Yesu Mbuye wathu inichita niuzile chindhu ichi. 32 Ngati, dala langa lidakali la chimundhupe, kujha kubulana kwanga ni wandhu yao adali ngati zinyama zokalipa pano pa Efeso kudakanithangatila chiyani? Ngati yao amwalila siahyuka basi, "Tidye ni kumwa ndande mawa sitimwalile."

33 Msadanyengeka, "Mabwenji woyipa uwananga ukhalo wako." 34 Ukani yambani kukhala bwino, nisiyani kuchita machimo. Akumojhi wanu siamujhiwilatu Mnungu, ichi nikukambilani ninjhoni yaikulu kwanu.

Thupi lo hyuka

35 Nambho mundhu wakhoza kufunjha, "Yao amwalila siahyukichidwe bwanji? Siakhale ni thupi la bwanji?" 36 Anyiimwe asabwabwa! Ukavyala mbeu, ngati siifa ndekuti siimela. 37 Yapo muvyala, muvyala mbeupe, ikhozeka ya ngano mbeu kapina ina, ni osati mmela wambhumbhu uwo uchokela pambuyo 38 Nambho Mnungu wazipacha mbeu thupi, ngati mujha wafunila iye, kila mbeu zipheza thupi la lokha.

39 Mathupi ya voumbidwa vonjhe siyalingana, nambho matupi ya wandhu yamtundu umojhi, ni matupi ya zinyama niyamtundu umojhi, ni matupi ya mbalame niyamtundu umojhi, ni matupi ya njhomba niyamtundu umojhi.

40 Yalipo mathupi ya kumwamba ni yapajhiko, kukhadwa kwa matupi ya kumwamba nikwina, ni kukhadwa kwa matupi ya pajhiko nikwina. 41 Kukhadwa kwa jhua, kulekana ni kukhadwa kwa mwezi, ni kukhadwa kwa mwezi ulekana ni ndhondwa ata ndhondwa zene zileka kwa kukhadwa.

42 Chimwecho ndeumo siikhalile ndhawi ya kuhyukichidwa. Ngati ijha mbeu, thupi likwililidwa mndhaka ni liwanangika nambho lihyukichidwa lili lokhadwa. 43 Thupi lizikidwa lilibe mbhavu ni silikhadwa, nambho lihyukichidwa lililokhadwa, lijha thupi la vyalidwa popande mbhavu, lihyukichidwa kwa mbhavu. 44 Thupi yapo lizikidwa, likhala thupi la kawaida, yapo lihyukichidwa ni thupi la chizimu, ni kuli thupi lakawaida, ni thupi la chizimu. 45 Malembo yalembedwa, "Mundhu woyamba Adamu wadali choumbidwa chamoyo" Nambho Adamu wothela iye ni Mzimu uyo wapacha wandhu umoyo. 46 Nambho lichogolela kukhalako, opande thupi lijha la chizimu ila thupi la kawaida, ndiipo likujha thupi lijha la chizimu. 47 Mundhu woyamba yaani Adamu, wadaumbidwa kwa dothi, wadachoka mndhaka, mundhu wakawili yaani Kilisito wadachoka kumwamba. 48 Wonjhe ali ajhiko la panjhi ali ngati mundhu uyo wadaumbidwa kwa dothi, anyiwajha ali akumwamba ali ngati yujha wadachoka kumwamba. 49 Ngati mujha talingana ni yujha wadaumbidwa kwa dothi, chimwecho ndeumo sitilingane ni yujha wachoka kumwamba.

50 Achabale nikamba chimwechi, chijha chachitidwa kwa thupi ni mwazi sichikhoza kulunjana ni Ufumu wa Mnungu, niicho chiwanangika sichikhoza kukhala chosawanangike.

51 Vechelani nikukambilani chisisi ichi, ife sitimwalila taonjhe nambho taonjhe siting'anamulidwe,

52 Mwachizulumukila, ndhawi ya mbetete yothela yapo siilile, yao amwalila siahyukichidwe, nafe siting'anamulidwe ni kukhala ni matupi yayo siyakufanjho. 53 Mate thupi lowanangika, ifunika livale kosawanangika, ni dala thupi la kumwalila ifunika livale osamwalila. 54 Chimwecho thupi ili lakuwanangika yapo silivale kosawanangika, nalo thupi la kumwalila yapo sili vale kosamwalila, ndeyapo lijha mawu lalembedwa silikwanile "Nyifa yawanangidwa kwa kuikhoza!"

55 "Kuli pati kukhoza kwa nyifa?

Kuli pati kuwawa kwa nyifa?"

56 Nyifa, ipata mbhavu ya kupweteka kuchoka kumachimo, ni machimo yapata mbhavu ya kupweteka kuchoka mthauko. 57 Nambho wayamikidwe Mnungu, iye watipacha kukhoza kwa kupitila Yesu Kilisito!

58 Chimwecho achabale wanga, imani nganganga msada tingizika. Mpunde kuichita njhito ya Ambuye, mate mjhiwa njhito ya Ambuye siitaika chajhe.

Veja também

Publicidade
1 Coríntios
Ver todos os capítulos de 1 Coríntios
Bíblia Online Bíblia Online

Bíblia Online • Versão: 2026-06-19_11-20-24-