1 Anya abale wanga, chipano nikamba ni anyiwajha alijhiwa thauko, simjhiwa kuti thauko likhala ni ulamulilo kwa mundhu wakakhala wamoyo? 2 Kwa chifani, wamkazi uyo wakwatiwa wamangidwa ni thauko ndhawi yonjhe yapo mmunake wakhala wamoyo, nambho mmunake wakamwalila, thauko limenelo silimmanganjho wamkazi mmeneyo. 3 Chimwecho wamkazi mmeneyo wakakwatiwa ni wammuna mwina ndhawi iyo mmunake wali wamoyo, siwatanidwe wachighololo. Nambho mmunake wakamwalila, wamkazi mmeneyo siwamangidwanjho ni thauko la ukwati, ni wakakwatiwa ni wammuna mwina siwatanidwa wachighololo. 4 Mchimwecho acha abale wanga, anyiimwe mdalekeledwa kuchokela thauko ngati umo mmakhalila kale, anyiimwe ni malo ya thupi la kilisito, chipano muli wa yujha wadahyukichidwa kuti mkhoze kuchita vichito vabwino ndande ya Mnungu. 5 Pakuti yapo timakhala ngati wandhupe umo akhalila, makumbilo yayo yadasongezeledwa ni machimo yamachita njhito mmatupi yathu, ni kupeleka nyifa. 6 Kalepo tidamangidwa ni thauko, nambho saino tamwalila pamojhi kilisito, mchimwecho tamasulidwa kuchokela mthauko. Chipano sitimtumikila Mnungu kwa njila ya kale ya kugwila thauko ilo lidalembedwa, nambho timtumikila Mnungu kwa njila ya chipano ya kuchogozedwa ni mzimu wa wake.
7 Chipano tikambe bwanji, tikambe kuti thauko ni mchimo? Notho! Nambho popande thauko, ine sinidakayajhiwa machimo ni chindhu chanji. Pakuti sinidakajhiwa mate yokumbila voipa, ngati thauko silidakakamba, "siudakhumbila" 8 Nambho kwa kutumila thauko limenelo, lidabala mkati mwanga kila mtundu wa khumbilo loipa. Pakupi popande thauko machimo ni chindhu cho mwalila. 9 Masiku ya mmbuyo yapo sinimalijhiwe thauko la Mnungu nimakhala umo nimafunila, nambho yapo nidajhiwa kuti thauko lifuna chiyani nidajhijhiwa kuti ine nili ni machimo. 10 Chimwecho thauko ilo limafunika kupeleka umoyo kwaine, lapeleka nyifa. 11 Pakuti machimo yadapata malo mthauko, chipano machimo yadaninyenga kwa njila ya lamulo limenelo ni kunipelekela lamulo la nyifa.
12 Chimwecho thauko lene lachoka kwa Mnungu, ni lamulo lene lachoka kwa Mnungu, ni yali ngati umo yafunikila ni yabwino 13 Bwanji ichi chilangiza chijha chili cha bwino chapeleka lamulo la nyifa yanga? Ata pang'ono! Ni chimwechi kuti machimo dala yaoneke padanga kuti ni machimo yachitumia chijha chili cha bwino ni kupeleka lamulo la nyifa yanga. Chimwecho machimo, kwa njila ya lijha lamulo, yadajhilangiza mokwanila umo ili yoipa kupunda.
14 Tijhiwa kuti thauko ni lachizimu, nambho ine osati wa Chizimu, ine naghulichidwa dala nikhale kapolo wa machimo. 15 Sinichijhiwa icho nichichita, pakuti chijha nichifuna sinichichita, nambho icho sinichifuna ndeicho nichichita. 16 Ngati nichita chijha sinichifuna ine kuchita, pamenepo nivomela kuti lijha thauko ni la bwino. 17 Nambo kwa uzene osati inenjho nichita chijha sinichifuna, nambho ni yajha machimo yakhala mkati mwanga nde yayo yanichita nichite icho sinichifuna. 18 Nijhiwa kuti palibe chabwino chalichonjhe mkati mwanga, kuchokana ni umundhu wanga, pakuti nifuna kuchita chindhu chabwino nambho sinikhoza kuchita. 19 Pakuti chijha chindhu chabwino nichifuna sinichichita, nambho choipa icho sinichifuna nde icho nichichita, 20 chipano ngati nichita icho sinichifuna, osati ine nichita nambho yajha machimo yakhala mkati mwanga nde yayo yachita.
21 Chipano najhiwa chimwechi, kuti nifuna kuchita chindhu chabwino, nambho nijhipeza kuti chijha chilichoipa nde ichonisangha. 22 Mumtima wanga, nilikondwela thauko la Mnungu. 23 Nambho niona kuti mkati mwanga kuli thauko lina ilo lichita njhito ilo lichuchana ni maganizo yanga ya bwino. Thauko limenelo linichita kukhala kapolo wa thauko la machimo yayo yachita njhito mthupi mwanga. 24 Chindhu ichi chinidandaula kupunda! Yani siwaniombole kuchokela mthupi lino linipeleka kunyifa? 25 Nimuyamika Mnungu uyo waniombola kupitila kwa Yesu kulisito!
Chimwechi nde umo nili ine, kwa njelu zanga, nilitumikila thauko la Mnungu, nambho kwa thupi langa liniguza kuchata machimo.