1 Basi mjhukulu wamkulu wadamfunjha Sitifano, "Bwanji, vindhu ivi ni vazene?"
2 Sitifano wadayangha, "Achaabale wanga ni achatate wanga, mnivechele! Mbuye wathu Ibulahimu yapo wadali wakali osapite kukhala ku Halani, Mnungu wa ulemelelo wadamuonekela iye ku Mesapotamiya. 3 Mnungu wadamkambila, ‘Asiye wandhu wako ni jhiko ni upite ku jhiko ilo sinikulangize.’ 4 Chimwecho Ibulahimu wadachoka mujhiko la Kalidayo ni kupita kukhala ku Halani. Atate wake Ibulahimu adamwalila, Mnungu wadamchocha kumeneko ni kujhanayo mu jhiko lino ilo anyiimwe mukhala ndhawi zino. 5 Mnungu siwadampache chilichonjhe mu jhiko lino, siwadampache ata pamalo poikapo mapazi yake. Nambho Mnungu wadaahidi kuti iye ni mbadwa wake pambuyo pake siakhale mjhiko muno, ata ngati nyengo imeneyo Ibulahimu wadalibe mwana. 6 Mnungu wadamkambila chimwechi, ‘Mibadwa yako siikhale ku jhiko la chilendo, siachitidwe kukhala akapolo ni kuchitidwa voipa kwa vyaka miya zinayi. 7 Nambho ine siniliwanange jhiko lijha silaavutiche ngati akapolo. Pambuyo pake siachoke mjhiko limenelo ni kunilambila pamalo yapa.’ 8 Ndiipo Mnungu wadachita chipangano ni Ibulahimu cha mdulidwe chikhale chizindikilo cha chipangano chimenecho. Nayo Ibulahimu wadambala Isaka ni kumchitila mdulidwe siku la nane pambuyo po badwa. Niiye Isaka wadamchita mdulidwe Yakobo mwana wake, ni Yakobo wadachita chimwecho kwa azee wathu khumi ni awili."
9 "Wana a Yakobo adamuonela njhanje mbale wao Yusufu, chimwecho adamgulicha kuti wakhale kapolo ku jhiko la Misili. Nambho Mungu wadali pamojhi ni iye. 10 Amnungu adamuombola kuchokela ku mavuto yake yonjhe yayo yadampata, ni wadampacha mwawi ni njelu yapo wadaima pamaso pa Falao, mfumu wa Misili, uyo wadamuika kuti wakhale mlamuli wa jhiko la Misili, ni mlamuli wa nyumba yonjhe ya chifumu. 11 Ndiipo kudali njala mu jhiko lonjhe la Misili ni Kaanani, iyo idapeleka kuvutika kwa kukulu. Ni achaatate wathu saadakhoze kupata chakudya. 12 Basi Yakobo wadavela kuti kuli chakudya ku Misili, wadaatuma wana wake yawo ali achambuyathu kukayendela uti. 13 Yapo adapita kakawili, Yusufu wadajhijhiwicha kwa achaabale wake, ni mfumu wa ku Misili wadaajhiwa achaabale a Yusufu. 14 Chimwecho, Yusufu wadapeleka uthenga kwa Yakobo atate wake, kwaakambila iwo ni wandhu wonjhe a kwake kuti ajhe ku Misili. Wonjhe pamojhi adali wandhu sabini ni asano. 15 Ndiipo Yakobo wadapita ku Misili, uko iye ni achanawake adafela. 16 Matupi yao yadabwezedwa ku Shekemu, uko adazikidwa mviliza ivo wadavigula Ibulahimu kuchokela kwa wana wa Hamoli kwa ndalama."
17 "Yapo idakwana ndhawi yokwanilicha yajha Mnungu wadaamuahidiya Ibulahimu, chiwelengo cha wandhu mujha mu Misili chidachuluka ni kukula. 18 Ndiipo wadachokela mfumu mwina uyo wadayamba kulamulila jhiko la Misili, uyo siwamamjhiwe Yusufu. 19 Mfumu mmeneyo wadaachita kuipa azee wathu ni pa kuwakakamiza kwaataya wana wao akhanda kuti afe. 20 Ndhawi imeneyo nde ndhawi iyo wadabadwila Musa, nayo wadali mwana uyo wadamuona kuti ni wabwino. Iye wadaleledwa kwa ndhawi ya miezi itatu. 21 Yapo adalepela kumbisa munyumba kwa ndhawi yaitali, adamuika kubwalo, ni mwali wa Falao wadamtenga ni kumulela ngati mwana wake mwenewake. 22 Musa wadayaluzidwa ekima zonjhe za ku Misili, wamakhoza kukamba bwino ni kuchita vindhu zosiyana siyana."
23 "Musa yapo wadakwana vyaka alobaini wadalamula kwaayendela achaabale wake a Izilaeli kupita kuona vindhu vanji ivo amachitidwa. 24 Kumeneko wadamuona mmojhi wa aizilaeli niwavutichidwa ni a Misili, chimwecho wadapita kumthandiza yujha Mwizilaeli, wadambula yujha m Misili ni kumupha kubwezela mbwezo. 25 Musa wamaganiza kuti achaabale wake adakajhiwa kuti Mnungu wamtumila kwaaombola, nambho anyiiwo sadajhiwe chimwecho. 26 Siku lidachatila Musa wadaakomana a Izilaeli awili naabulana, wadayesa kwaavanichana pakwaakambila, ‘Anyiimwe ni achabale, bwanji mufuna kupwetekana mwachinawene?’ 27 Nambho mwina yujha wamambula mnjake wadamkangha Musa kutali, wadamfunjha, ‘Yani uyo wakuika iwe kukhala mchogoleli ni mlamuli wathu? 28 Bwanji, ufuna kunipha ngati umo udamphela yujha Mmisili jhulo?’ 29 Musa yapo wadavela chimwechi, wadathawa ni kupita kukhala mjhiko la Midiyani. Kumeneko Musa wadabala wana awili waachimuna.
30 "Yapo vidapita vyaka alobaini, atumiki a kumwamba a Mnungu adamchokela Musa mnjila ya fukutu ilo limakwelela moto kuphululu kujha pafupi ni phili la Sinayi. 31 Musa wadazizwa yapo wadaona vindhu vimenevo, wadasendelela pafupi ni fukutu lijha kuti waone bwino. Nambho wadavela mvekelo wa Ambuye niakamba, 32 ‘Ine ni Mnungu wa azee wako a kale, Mnungu wa Ibulahimu, Isaka ni Yakobo.’ Musa wadatendhemela kwa mandha ni wadayese kupenyanjho. 33 Mnungu wadamkambila Musa, ‘Vula malapasi yako, pakuti pamalo pano waima ni pamalo Poyela. 34 Nayaona mavuto ya wandhu wanga kujha ku Misili. Navela chililo chao, chipano najha kwaombola. Basi chipano, sinikutume ku jhiko la Misili.’"
35 "Musa mmeneyo nde yujha wandhu a Ku Izilaeli adamkana yapo adakamba, ‘Yani uyo wakuika iwe kukhala mchogoleli ni mlamuli wathu?’ Kwanjila ya yujha Mtumiki wa Kumwamba wa Mnungu uyo wadamchokela Musa ku fukutu limakwelela moto, Mnungu wadamtuma Musa wakhale mchogoleli ni muomboli. 36 Nde uyo wadaachogoza wandhu kuchoka ku Misili, niwachita vodabwicha ni vozizwicha mu Misili ni pa Nyanja ya Shamu, ni muphululu mu ndhawi ya vyaka alobaini. 37 Musa nde uyo wadaakambila wandhu a ku Izilaeli, ‘Mnungu siwakusanghulileni mlosi ngati umo wanitumila ine, ni siwachokele pakati panu mwachinawene.’ 38 Aizilaeli yapo adasonghana kujha ku phululu, Musa nde uyo wadalipo kumeneko ngati mthenga pakati pa azee wathu ni yujha mtumiki wa kumwamba wa Mnungu adakamba naye kuphili la Sinai, ndeuyo wadapachidwa mau yayo yapeleka umoyo."
39 "Nambho azee wathu adakana kumuvela Musa, adambwanyizila kutali ni kufuna kuti abwelelenjho ku Misili. 40 Chimwecho adamkambila Aloni, ‘Tikonjele minungu iyo siitichogoze. Pakuti sitijhiwa icho chamchokela Musa uyo watichogoza kuchokela ku Misili!’ 41 Pamenepo nde yapo adajhikonjela chiboliboli cha mwana wa ng'ombe, adachichochela njhembe ni kuchita phwando kuchikondwela chijha chiboliboli. 42 Ndipo Mnungu wadaasiya ni kwaachita ajhilambila ndhondwa za kumwamba ngati umo yalembedwela muchikalakala cha alosi,
‘Anyiimwe wandhu a ku Izilaeli!
Osati ine mdanichochela njhembe yophyeleza
kwa vyaka alobaini mu phululu?
43 Anyiimwe nde mudatenga hema la mnungu Moleki,
ni viboliboli va ndhondwa ya mnungu wanu Lefani,
viboliboli ivo mudavikonja, nde ivo mdavilambila.
Chimwecho, inenjho sinikupelekeni ku ukapolo kutali kupitilila jhiko la Babiloni.’"
44 Achaatate wathu adali ni hema lijha limalangiza kuti Mnungu wali pamenepo. Lidakonjedwa ngati umo Mnungu wadamkambila Musa wachite, kuchokana ni umo wadalangizidwa kuti walikonje. 45 Pambuyo pake, azee wathu wajha adalandilana hema limenelo ayiiwo kwa anyiiwo mbaka Yoshuwa yapo wamachogoza, adalanda jhiko kuchokela kwa maiko yajha yadatopoledwa ni Mnungu pamaso pao. Hemalo lidakhala mjhiko limenelo mbaka pa ndhawi iyo Daudi. 46 Daudi wadakondeledwa ni Mnungu, ni wadapembha Mnungu kuti wamloleze wammangile nyumba umo iye ni Aizilaeli wonjhe akhoza kumlambila. 47 Nambho Solomoni nde uyo wadamanga nyumba ya Mnungu. 48 Ata chimwecho, Mnungu wamkulu wa Kumwamba siwakhala mnyumba yomangidwa ni manja ya mundhu, ngati umo mlosi wakambila,
49 "Ambuye akamba, ‘Kumwamba ni mpando wanga wachifumu,
ni pajhiko lapanjhi ni malo ya kuikapo miyendo yanga.
Nyumba yamtundu wanji iyo simunimangile ine?
Kapina malo yanga yopumulilamo siyakhale yati?
50 Bwanji, vindhu vonjhevi sinidavimange ine kwa manja yanga?’"
51 Sitefano wadaendekela kukamba, "Anyiimwe ni wandhu a mbwinya, mitima ni makutu yanu yali ngati wandhu yawo samjhiwa Mnungu, ndhawi zonjhe simusiya kulimbana ni Mzimu Woyela, ngati umo adachitila azee wanu akale. 52 Bwanji, pali mlosi yuti uyo achambuye wanu saadamvutiche? Adaapha yawo Mnungu wadatuma akauzile kujha kwake yujha wovomelezeka. Namwenjho muli wandhu yawo mumunga'anamuka ni kumpha. 53 Anyiimwe nde anyiyawo mudalandila thauko, ilo lidapelekedwa ni atumiki akumwamba a Mnungu, nambho simchita ngati umo ifunikila."
54 Anyiwajha Azee a bwalo yapo adavela chimwechi, adakwiya kupunda adamkukutila mano kwambwayi Sitefano. 55 Nambho Sitifano, wali wojhala Mzimu Woyela, wadapenya kumwamba ni wadaona ulemelelo wa Mnungu, ni Yesu wadakhala ku malo ya ulemu ya Amnungu. 56 Wadaakambila, "Vechelani! Niona kumwamba kwachekuka ni Mwana wa Mundhu wakhala kujhanja la kwene la Mnungu!"
57 Nambho anyiiwo adapunda kubula phokoso lalikulu, adacheka makutu, ndiipo wonjhe adamlumbhila kwa pamojhi. 58 Adamtaya kubwalo kwa mujhi ni kuyamba kumponya miyala. Wajha amboni adaika njhalu zao pa miyendo ya mnyamata mmojhi uyo wamatanidwa Saulo kuti wachite ulonda. 59 Yapo amaendekela kumpmonya miyala, Sitifano wadapembhela, "Ambuye Yesu, landilani mzimu wanga!" 60 Wadagwada ni kulila kwa mvekelo wa waukulu, "Ambuye, musadalamula wandhu yawa kwa machimo yaya." Yapo wadamaliza kukamba chimwecho, wadamwalila.