1 Poolo wadakamba achaabale wanga ni anyaatate wanga munivele bwino umo nijhiteteza pachogolo panu! 2 Yapo adamvela niwaakambila mu Chihebulaniya, adapunda kukhala chete, ni Poolo wadayendekela kukamba,
3 "Ine ni Muyahudi, nidabadwila ku Taliso mmujhi wa Kilikiya. Nambho nakulilila muno mu Yelusalemu ine ni oyaluzidwa wa Gamalieli. Nidayaluzidwa kuchata mokwana Thauko la azee wathu akale. Nidajhichocha mwa mtima wanga wojhe kwa Mnungu ngati umo mwajhichochochela anyiimwe pano. 4 Nidavuticha ni kwa ipha wandhu wajha adachata njila ya ukhalo uwu. Nidaagwila wachimuna ni wachikazi ni kwamanga mndende. 5 Mjhukulu wamkulu ni bwalo lonjhe la azee Achiyahudi akhoza kukuchimikizilani nghani izi. Kuchokela kwanyiiwo nidalandila kalata iyo idalembedwa ni wajha abale a Chiyahudi aku Damasiko, ni nidapita kujha kwaagwila wandhu ni kujhanawo ku Yelusalemu uku amangidwa maunyolo kuti alangidwe."
6 "Chimwecho yapo nidali paulendo pafupi kufika ku damasiko, ngati sasita usana chimwechi, dangalila long'azimila kupunda kuchokela kumwamba lidaniwalila kunizungulila madela yonjhe mwachizulumukila. 7 Nidagwa panjhi ni nidavela mvekelo niunikambila, ‘Saulo, Saulo! Ndande yanji univuticha?’ 8 Nidayangha, ‘Imwe ayani, Ambuye?’ Mvekelo udaveka, ‘Ine Yesu wa ku Nazaleti, uyo univuticha.’ 9 Wandhu yawo adali niine adaliona dangalila, nambho saadauvele mvekelo wa uyo wamakamba nane. 10 Ndiipo nidafunjha, ‘Ifunika nichite chiyani, Ambuye?’ Ambuye adaniyangha, ‘Ima ni upite ku Damasiko. Kumeneko sinikukambile yonjhe yayo Mnungu waikilidwa uyachite.’ 11 Nidali wosapenya ndande ya lijha dangalila lalikulu lidaniwalila, ni athandizi wanga adanigwila jhanja ni kupita nane ku Damasiko."
12 "Kujha ku Damasiko kudali mundhu uyo wamatanidwa Ananiya, mundhu uyo wagwila thauko ni wamalemekezedwa ni Ayahudi wonjhe yawo amakhala ku damesiko. 13 Iye wadajha kwa ine, wadaima pafupi ni ine ni kukamba, ‘Mbale wanga Saulo, penyanjho!’ Pampajha maso yanga yadayamba kupenyanjho nane nidamuona Ananiya. 14 Wadakamba, ‘Mnungu wa achaatate wathu wakusangha iwe kuti ujhiwe vindu ivo avifuna uchite. Wakusangha iwe kuti umuone Mtumiki wake ni kumvela iye. 15 Pakuti iwe siwakambile wandhu yajha wayaona ni kuyavela. 16 Chipano siufunika kulindila ndhawi yaitali. Ima ubatizidwe ni kuelechedwa machimo yako dala ulekeleledwe kwa kukhulupilila jhina la Ambuye.’"
17 "Nidabwelela ku Yelusalemu, nambho yapo nidalikupembhela pa Nyumba ya Mnungu, nidaona masombhenya. 18 Nidaaona Ambuye, uku nianikambila, ‘Uchite msanga uchoke mu Yelusalemu, pakuti wandhu anyiyawa saaulandila umboni wanga uwo siuchoche.’ 19 Ine nidayangha, ‘Ambuye, anyiiwo ajhiwa bwino kuti nidapita mmanyumba yonjhe yokomanilana Ayahudi ni kwaabula yawo akukhulupililani imwe. 20 Yapo wamaphedwa Sitifano mmboni wako, ine namwene nidali pampajha ni nidavomelezana kuti wapedwe niine nde nimalonda njhalu zawajha akupha’ 21 Ambuye adanikambila, ‘Pita, pakuti sinikutume kutali kwa wandhu osati Ayahudi.’"
22 Mbaka yapa, wajha wandhu amamvechela, nambho yapo wadakamba mawu yaya, ndiipo adakweza mvekelo wao niakamba mundhu mmeneyo waphedwe mundhu, ndande yake siwafunika kukhala wamoyo! 23 Anyiiwo amabula phokoso ni kuvula njhalu zao ni kufulila lifumbi kumwamba. 24 Ndiipo yujha wamkulu wa asikali wadalamula kuti amgwile Poolo ni kumlovya mkati mwa nyumba ya asikali, niwadalamula kuti wabulidwe mikwapulo, uku niwamfujha ndande yanjhi Ayahudi abula pokoso. 25 Nambho yapo adathommanga vingwe kuti amkwapule, Poolo wadamfunjha mkulu wa gulu la asikali uyo wadaima pampajha pafupi ni iye, "Bwanji, thauko la jhiko la Aloma lilola kumbula mundhu wakuloma wakali osalamulidwe?"
26 Wamkulu yujha yapo wadavela chimwechi, wadapita kwa wamkulu wa asikali ni kumkambila, "Ufuna kuchita chiyani? Uyu mundhu ni Mloma!"
27 Chimwecho wamkulu wa asikali yujha wathamangila kwa Poolo ni kumfunjha, "Nikambile, iwe ni mundhu wa ku Loma?"
Poolo wadayangha, "Yetu, ine mundhu wa ku Loma."
28 Wamkulu wa asikali wadakamba, "Ine nane ni Mloma kwa kulipila ndalama zambili."
Poolo wadayangha, "Nambho ine ni Mloma wobadwa."
29 Kankamojhi wandhu wajha amafuna kumfunjha uku ni ambula, pampajha adachoka ni yujha wamkulu wa asikali wadaopa kupunda yapo wadajhiwa kuti Poolo wadali Mloma wadaopa ndande wadathommanga maunyolo.
30 Siku lakawili wamkulu wa asikali wamafuna kujhiwa ndande iyo Ayahudi amafuna kumpacha mlandu Poolo. Chimwecho wadammasula yajha maunyolo ni wadalamula ajhukulu wakulu na azee a bwalo lalikulu lonjhe kukomana pamojhi. Ndiipo wadamtenga Poolo ni kumuika waime pachogolo pao.