1 Wandhu yawo adamkhulupilila Mnungu ku Antiokia wina adali alosi ni oyaluza, pakati pao padali Banaba, Simioni uyo watanidwa Wakuda, Lukiya uyo wachokela ku mujhi wa Kilene ni Saulo ni Manaeni uyo wadaleledwa pamojhi ni mfumu Helode Antipasi. 2 Yapo amampembha Mnungu ni kumanga kudya, Mzimu Woyela udaakambila, "Nipatulileni Banaba ni Saulo, kuti achite njhito iyo naatanila kuchita."
3 Yapo adamaliza kumanga kudya ni kupembhela, anyiiwo adaasanjika manja Banaba ni Saulo ni kwasiya ajhipita.
4 Banaba ni Saulo yapo adatumidwa ni Mzimu Woyela, adachikilila ku Seleukiya ni kupitanjho mbaka ku chilumba cha Kipulo. 5 Yapo adafika mmujhi wa Salami, adalalikila uthenga wa Mnungu munyumba zaokomanilana Ayahudi. Yohana uyo wamatanidwanjho Maluko wamatokwathangatila kuchita njhito yawo ya utumiki.
6 Adapita kumalo yambili mbaka kufika ku chilumba icho chitanidwa Pafo, kumeneko adakomana ni Myahudi mmojhi mfiti jhina lake Bali yesu, Myahudi uyo wamajhichita kuti ni mlosi. 7 Mmeneyo wadali bwenji wa Segiyo Poolo, mundhu wanjelu kupunda, uyo wadali wamkulu wa chilumba. Iye wadaalalika Banaba ni Saulo kufuna kuti wavele mau la Mnungu. 8 Nambho Elima yujha mfiti, Elima pachigiliki mate yake, "Wochucha." Wamafuna kumchucha wamkulu wa chilumba chijha kuti siwadamkhulupilila Yesu. 9 Ndiipo Saulo uyo watanidwa Poolo, wadajhala Mzimu Woyela, wadampenyechecha Elima ni kukamba, 10 "Iwe mwana wa Satana! Iwe ni mdani wa chilichonjhe icho chili cha uzene. Iwe wajhala mthila wa kila mtundu, ni nyengo zambili uyesa kuung'anamula uzene wa Ambuye kukhala mthila! 11 Chimwecho, jhanja la Ambuye silikuwanange, siukhale wosapenya ni siuliona jhuwa kwa ndhawi."
Pampajha Elima wadaona chidima nichivinikila maso yake, wadayamba kumfunafuna mundhu wakumgwila jhanja kuti wamchogoze. 12 Wamkulu wa chilumba yujha yapo wadaona yayo yadachitika, wadamkhulupilila Yesu, pakuti wadadabwa kupunda pa mayaluzo yanghani za Ambuye Yesu.
13 Ndiipo Poolo na achanjake adakwela sitima kuchokela ku Pafo ni kupita ku Pega mmujhi wa Pamfiliya, nambho Yohana wadaasiya ni kupita ku Yelusalemu. 14 Anyiiwo adayendekela kuyenda kuchokela ku Pege mbaka kufika ku Pisidiya mmujhi wa Antiyokia. Siku Lopumula anyiiwo adapita ku nyumba yokamanilana Ayahudi ni kukhala. 15 Yapo adamaliza kusoma chikalakala cha thauko la Musa ni mumalembo ya alosi a Mnungu, waakuluakulu a nyumba yokomanilana Ayahudi adaatumila anyiiwo uthenga, "Achaakulu wathu Banaba ni Saulo, tifuna kuti mukambe ni wandhu ngati muli ni mau yaliyonjhe yakwaathila mtima, basi muyakambe." 16 Poolo wadaima ni kwapungila jhanja, ni kuyamba kukamba,
"Anyiimwe a Izilaeli anjanga ni anyiimwe mwaonjhe yawo mumlambila Mnungu, niveleni! 17 Mnungu wa wandhu a ku Izilaeli waasangha azee wathu ni kwaachita wandhu kukhala jhiko lalikulu yapo adali kujha ku Misili. Mnungu wadaachocha ku Misili kwa mbhavu zake zazikulu, 18 naye Mnungu wadaalimbila mtima mu phululu kwa vyaka alobaini. 19 Mnungu wadayawananga mafuko saba ya mujhiko la Kanaani, ni kwaapacha wandhu jhiko limenelo kuti likhale lao." 20 Yaya yonjhe yadachitika mkati mwa vyaka miya nne ni amsini.
"Wadaapacha alamuli kuti waachogoze mbaka nyengo ya mlosi Samweli. 21 Ndiipo wandhu adafuna kuti apachidwe mfumu. Nayo Mnungu wadaapacha Saulo mwana wa Kishi, wa mtundu wa Benyamini kukhala mfumu wao kwa vyaka alobaini. 22 Mnungu yapo wadamchocha Saulo muulamulilo, Mnugu wadamchita Daudi kukhala mfumu wao. Ichi nde icho wadakamba Mnungu, ‘Namuona Daudi mwana Yese, nde mundhu uyo waukondwelecha mtima wanga, uyo siwakwaniliche vonjhe ivo nifuna kuvichita.’ 23 Kuchokela mu ubazi wa Daudi, Mnungu waapelekela wandhu a Izilaeli muomboli, iye nde Yesu, ngati umo wadaahidila. 24 Yesu yapo wadali wakali osayamba njhito yake, Yohana Mbatizi wadalalikila wandhu wonjhe a Izilaeli kuti alape machimo yao ni kubatizidwa. 25 Yapo Yohana Mbatizi wadali pafupi kumaliza njhito yake, wadaakambila wandhu, ‘Mganiza ine ni yani? Ine osati Muomboli uyo mumlindilila. Nambho vechelani! Iye watokujha mmbuyo mwanga, ni sinikhoza kumasula vingwe va malapasi yake.’"
26 "Achabale wanga a Izilaeli, wana a Ibulahimu, ni wandhu yawo osati Ayahudi yawo amlambila Mnungu, uthenga uwu wa uwomboli wapelekedwa kwa wandhu onjhe! 27 Pakuti wandhu yawo akhala mu Izilaeli ni achogoleli wao saadajhiwe kuti Yesu ni Muomboli, kapina kuvela mau ya ulosi yayo yamasomedwa kila Siku Lopumulila. Nambho mau yamenyo yakwanilichidwa kwa kummulamula kumpha Yesu. 28 Ata chimwecho, anyiiwo adalepela kupata ndande yomuphela Yesu, mmalo mwake adampembha Pilato kuti wamphe. 29 Yapo adatho mpha kwa kumpachika pamtanda, adamchicha ni kumuika mu mbhanga. 30 Nambho Mnungu wadamuhyukicha, 31 ni kwa masiku yambili, iye wadaonekela wajha amayenda maulendo pamojhi ni iye kuchokela ku Galilaya kupita ku Yelusalemu. Chipano anyiiwo ni amboni wake kwa wandhu a Izilaeli. 32 Nafe takupelekelani Uthenga Wabwino wadakambila Mnungu azee wathu, 33 chipano wayakwanilicha kwa ife wana wake, yawo tili mbadwa wao pakumhyukicha Yesu. Ngati umo yalembedwele mchikalakala cha Zabuli,
‘Iwe ni mwana wanga,
lelo nakhala Atate wako.’
34 Pakuti umu nde umo wadakambila Mnungu nghani za kumuhyukicha Yesu, kuti siwadaolela mmbhanga,
‘Sinikupache mwawi woyela ni wauzene
uwo nidaakambila kwa Daudi.’
35 Ngatinjho umo wakambila mumalo yina ya chikalakala cha Zabuli,
‘Simumsiya mbowa wanu woyela kuti waole.’
36 Nambho siyadachitike chimwecho kwa Daudi, pakuti Daudi wadamtumikila Mnungu pa ndhawi yake, ndipo wadamwalila, wadazikidwa mumbhanga iyo idali pafupi ni azee wake, ni thupi lake lidaola. 37 Nambho yujha uyo Mnungu wadamhyukicha siwadaole. 38 Chimwecho, achaabale wathu a Izilaeli mujhiwe kuti kwa njila ya Yesu, uthenga wa kulekeleledwa machimo ulalikidwa kwanu. 39 Mundhu waliyonjhe uyo wamkhulupilila Kilisito siwalekeleledwe machimo yake. Chindhu icho sichidakakhozeka kwa kulemekeza thauko la Musa. 40 Chipano mukhale maso kuti yajha yadakambidwa ni alosi siyadachitika kwanu,
41 ‘Vechelani, anyiimwe wandhu avipongwe! Mkazizwe ni kumwalila!
Pakuti icho nichita lelo
ni chindhu icho simuchikhulupilila,
ata ngati mundhu mwina wakakufotokozeleni!’"
42 Yapo Poolo ni Banaba amatuluka mu nyumba yokomanilana Ayahudi, wandhu wajha adaapembha ajhenjho Siku Lopumula likujha kuti waakambile vambili va nghani ya vindhu vimenevo. 43 Wandhu yapo adachoka pa nyumba yokomanilana Ayahudi, Ayahudi ni wandhu osati Ayahudi ambili yawo adalowa mchipembezo cha chiyahudi wadaachata Poolo ni Banaba, nawo adakamba nawo ni kwaathila mtima kuti ayendekele kukhulupilila mwawi wa Mnungu.
44 Siku Lopumulila ilo lidachata, wandhu ambili a mmujhi ujha adajha kuvechela nghani zabwino za Yesu. 45 Ayahudi yapo adaona gulu la wandhu, adachita njhanje, nikunena mau ya vipongwe kuchuchana ni mau yajha wamakamba Poolo ni kumtukwana. 46 Nambho Poolo ni Banaba adakamba mau popande mandha, "Idafunika kuti mau la Mnungu likambidwe kwanu poyamba, nambho mwalikana, chimwecho mwajhilanga mwachinawenewake simufunika kukhala amoyo muyaya, tikusiyani ni kupita kwa wandhu osati Ayahudi. 47 Ili nde lamulo ilo atipacha Ambuye,
‘Nakuchitani kukhala dangalila kwa wandhu osati Ayahudi,
kuti wandhu onjhe ajhiko la panjhi aomboledwe.’"
48 Wandhu osati Ayahudi yapo adavela chimwecho, adakondwa ni adautamanda uthenga wa Mnungu, ni wajha adasanghidwa ni Mnungu kuti akhale ni umoyo wa muyaya, adaakhulupilila Ambuye Yesu.
49 Mau la Ambuye lidaenela pa malo pajha ponjhe. 50 Nambho Ayahudi wadaakhwilizila achogoleli waachikazi yawo amlambila Mnungu ni amaudindo ni wandhu wojhiwika mu mujhi. Adayamba kwaavuta Poolo ni Banaba ni kwaatopola achoke malo yao. 51 Ndiipo, Poolo ni Banaba adakung'undha malifumbi ya mmyendo mwao kulangiza kwaonya ni kupita kumujhi wa Ikoniyo. 52 Nambho oyaluzidwa a Yesu adakondwa ni adachogozedwa ni Mzimu Woyela.