1 Kila mundhu wafunika kwavela yawo ali ni ulamulilo aselikali, pakuti alamuli wonjhe achokela kwa Mnungu, ni anyiiwo ali ni ulamulilo aikidwa ni Mnungu 2 Uyo waachucha yawo ali ni ulamulilo waachucha lamulo la Mnungu, ni anyiawo achita chimwecho salamulidwe achinawene. 3 Pakuti alamuli sapeleka mandha kwa wandhu yawo achita vabwino, nambho apeleka mandha kwa wandhu yao achita voipa. Chipano ufuna siudamwopa mundhu uyo wali ni ulamulilo? Chita vabwino niiwe siwakuelekele. 4 Pakuti iye ni mtumiki wa Mnungu wachita njhito ndande ya kukuthangatila iwe. Nambho ukachita voipa, panepo ifunika waope, pakuti ali ni mbhavu zakukulanga. Iye ni mtumiki kwa Mnungu, wali ndande ya kwalangiza mbhwayi yake anyiwajha achita voipa. 5 Chipano ifunika kwaavechela ali ni ulamulilo, osati ndande yoopa mbhwayi ya Mnungu, nambho ndande mujhiwa chimenecho chindhu chabwino kuchichita.
6 Ndande imeneyo anyiimwe mchocha malipilo, pakuti achogoleli ameneo amtumikila Mnungu, uku niachita njhito yao. 7 Apacheni wandhu chijha chifunika apachidwe, yawo afunika kupachidwa malipilo apacheni, yawo afunika kwapacha msongho apachidwe, ni yawo afunika alemekezedwe apacheni ulemu.
8 Simdadaidwa chindhu ni Mundhu waliyonjhe, nambho mjhikondana. Uyo wamkonda mnjake wakwanilicha thauko la Mnungu. 9 Pakuti yalembedwa mlamulo, "Siudachita chigololo, siudapha, siudaba, siudakhumbila" Ina yonjhe zili mlamulo ili limojhi, "Mkonde mnjakoi ngati umo ujhikondela umwene." 10 Uyo wamkonda mnjake siwakhoza kumchitila chindhu choipa. Chimwecho chikondi nde kuvela thauko lonjhe.
11 Anyiimwe mchite chimwechi uku ni mzijhiwa nyengo izo tilinazo. Ndhawi youka kuchokela kulitulo yatowandikila, pakuti ndhawi ya uwomboli watu yawandikila kupunda kusiyani ni poyamba yapo tidakhulupilila. 12 Usiku watha ni usana wawandikila. Chipano tisiye vindhu vonjhe va kumdima, tutenge vida ngati Asikali akonjeka kubulana mu dangalila. 13 Sitidakhala wandhu ochita mapwando ya kumwa mowa ni kulojhela, ukazuzu, chigololo, ndewo ni njhanjhe. 14 Ganizilani nikuchita ngati umo Ambuye Yesu Kilisito adachitila.